Aroma 14 BL92

Cipiriro ca pa ofoka

1 Ndipo iye amene ali wofoka m'cikhulupiriro, mumlandire, koma si kucita naye makani otsutsana ai.

2 Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofoka angodya zitsamba.

3 Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira.

4 Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wace? iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wace wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.

5 Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzace; wina aganizira kuti masiku onse alingana. Munthu ali yense akhazikike konse mumtima mwace.

6 Iye wakusamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye, pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya, mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu.

7 Pakuti palibe mmodzi wa ife adzikhalira ndi moyo yekha, ndipo palibe mmodzi adzifera yekha.

8 Pakuti tingakhale tiri ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; cifukwa cace tingakhale tiri ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ace a Ambuye.

9 Pakuti, cifukwa ca ici Kristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo.

10 Koma iwe uweruziranji mbale wako? kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? pakuti ife tonse tidzaimirira ku mpando wakuweruza wa Mulungu.

11 Pakuti kwalembedwa,Pali moyo wanga, ari Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine,Ndipo malilime onse adzabvomereza Mulungu,

12 Cotero munthu ali yense wa ife adzadziwerengera mlandu wace kwa Mulungu.

Kusamalirana

13 Cifukwa cace risaweruzanenso wina mnzace; koma weruzani ici makamaka, kuti munthu asaike cokhumudwitsa pa njira ya mbale wace, kapena compunthwitsa.

14 Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe cinthu conyansa pa cokha; koma kwa ameneyo aciyesa conyansa, kwa iye cikhala conyansa.

15 Koma ngati iwe wacititsa mbale wako cisoni ndi cakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi cikondano. Usamuononga ndi cakudya cako, iye amene Kristu adamfera.

16 Cifukwa cace musalole cabwino canu acisinjirire,

17 Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala cakudya ndi cakumwa, koma cilungamo, ndi mtendere, ndi cimwemwe mwa Mzimu Woyera.

18 Pakuti iye amene atumikira Kristu mu izi akondweretsa Mulungu, nabvomerezeka ndi anthu.

19 Cifukwa cace tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzace.

20 Usapasule nchito ya Mulungu cifukwa ca cakudya. Zinthu zonse ziri zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.

21 Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusacita cinthu ciri conse cakukhumudwitsa mbale wako.

22 Cikhulupiriro cimene uli naco, ukhale naco kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu. Wodala ndiye amene sadziweruza mwini yekha m'zinthu zomwe iye wazibvomereza.

23 Koma iye amene akayika-kayika pakudya, atsutsika, cifukwa akudya wopanda cikhulupiriro; ndipo cinthu ciri conse cosaturuka m'cikhulupiriro, ndico ucimo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16