1 Nanga kodi simudziwa, abale, pakuti ndilankhula ndi anthu akudziwa lamulo, kuti lamulolo licita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo?
2 Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wace wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.
3 Ndipo cifukwa cace, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wace wamoyo, adzanenedwa mkazi wacigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; cotero sakhala wacigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
4 Cotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku cilamulo ndi thupi la Kristu; kuti mukakhale ace a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso,
5 Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za macimo, zimene zinali mwa cilamulo, zinalikucita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso,
6 Koma tsopano tinamasulidwa kucilamulo, popeza tinafa kwa ici cimene tinagwidwa naco kale; cotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'cilembo cakale ai.
7 Pamenepo tidzatani? Kodi cilamulo ciri ucimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira ucimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira cilakolako sicikadati cilamulo, Usasirire;
8 koma ucimo, pamene unapeza cifukwa, unacita m'kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo ucimo uli wakufa.
9 Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, ucimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.
10 Ndipo lamulo, limene linali Iakupatsa moyo, ndinalipeza lakupassa imfa.
11 Pakuti ucimo, pamene unapeza cifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo.
12 Cotero cilamulo ciri coyera, ndi cilangizo cace ncoyera, ndi colunaama, ndi cabwino.
13 Ndipo tsopano cabwino cija cinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma ucimo, kuti uoneke kuti uli ucimo, wandicitira imfa mwa cabwino cija; kuti ucimo ukakhale wocimwitsa ndithu mwa lamulo.
14 Pakuti tidziwa kuti cilamulo ciri cauzimu; koma ine ndiri wathupi, wogulitsidwa kapolo wa ucimo.
15 Pakuti cimene ndicita sindicidziwa; pakuti sindicita cimene ndifuna, koma cimene ndidana naco, ndicita ici.
16 Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, ndibvomerezana naco cilamulo kuti ciri cabwino.
17 Ndipo tsopano si ine ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.
18 Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala cinthu cabwino; pakuti kufuna ndiri nako, koma kucita cabwino sindikupeza.
19 Pakuti cabwino cimene ndicifuna, sindicicita; koma coipa cimene sindicifuna, cimeneco ndicicita.
20 Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, si ndinenso amene ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.
21 Ndipo cotero odipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna cabwino, coipa ciriko.
22 Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi cilamulo ca Mulungu:
23 koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m'ziwalo zanga.
24 Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi?
25 Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu. Ndipo cotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira cilamulo ca Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la ucimo.