1 Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa, Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
2 Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.
3 Pakuti ndi cisomo capatsidwa kwa ine, ndiuza munthu ali yense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga, Mulungu anagawira kwa munthu ali yense muyeso wa cikhulupiriro,
4 Pakuti monga m'thupi limodzi tiri nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo siziri nayo nchito imodzimodzi;
5 comweco ife, ndife ambiri, tiri thupi limodzi mwa Kristu, ndi ziwalo zinzace, wina ndi wina.
6 Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;
7 kapenayakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;
8 kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo, acite ndi kukondwa mtima.
9 Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana naco cabwino.
10 M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;
11 musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani Ambuye;
12 kondwerani m'ciyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani cilimbikire m'kupemphera,
13 Patsani zosowa oyera mtima; cerezani aulendo.
14 Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere.
15 Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.
16 Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace. Musasamalire zinthu zazikuru, koma phatikanani nao odzicepetsa, Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
17 Musabwezere munthu ali yense coipa cosinthana ndi coipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.
18 Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.
19 Musabwezere coipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
20 Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a mota pamutu pace.
21 Musagonje kwa coipa, koma ndi cabwino genietsani coipa.