1 Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu;
2 amene ife tikhoza kulowa naye ndi cikhulupiriro m'cisomo ici m'mene tirikuunamo; ndipo tikondwera m'ciyembekezo ca ulemerero wa Mulungu.
3 Ndipo si cotero cokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti cisautso cicita cipiriro; ndi cipiriro cicita cizolowezi;
4 ndi cizolowezi cicita ciyembekezo:
5 ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.
6 Pakuti pamene tinali cikhalire ofok a, pa nyengo yace Kristu anawafera osapembedza.
7 Pakuti ndi cibvuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.
8 Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.
9 Ndipo tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.
10 Pakuti ngati, pokhala ife adani ace, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wace, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wace.
11 Ndipo si cotero cokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene talandira naye tsopano ciyanjanitso.
12 Cifukwa cace, monga ucimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa ucimo; cotero imfa inafikira anthu onse, cifukwa kuti onse anacimwa.
13 Pakuti kufikira nthawi ya lamulo ucimo unali m'dziko lapansi; koma ucimo suwerengedwa popanda lamulo.
14 Komatu imfa inacita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanacimwa monga macimwidwe ace a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo.
15 Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa cifukwa ca kulakwa kwammodziyo, makamaka ndithu cisomo ca Mulungu, ndi mphatso yaulere zakucokera ndi munthu mmodziyo Yesu Kristu, zinacurukira anthu ambiri.
16 Ndipo mphatso siinadza monga mwa mmodzi wakucimwa, pakuti mlandu ndithu unacokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere icokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.
17 Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inacita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kucuruka kwace kwa cisomo ndi kwa mphatso ya cilungamo, adzacita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Kristu.
18 Cifukwa cace, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; comweconso mwa cilungamitso cimodzi cilungamo ca moyo cinafikira anthu onse.
19 Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ocimwa, comweco ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.
20 Ndipo lamulo linalowa moyenjezera, kuti kulakwa kukacuruke; koma rl pamene ucimo unacuruka, pomwepo cisomo cinacuruka koposa;
21 kuti, mongaucimo unacita ufumu muimfa, comweconso cisomo cikacite ufumu mwa cilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.