Aroma 6 BL92

Kristu anatityolera mphamvu ya zotpa

1 Cifukwa cace tidzatani? Tidzakhalabe m'ucimo kodi, kuti cisomo cicuruke?

2 Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala bwanji cikhalire m'menemo?

3 Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?

4 Cifukwa cace tinaikldwa m'manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.

5 Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi iye m'cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m'cifani'Zidwe ca kuuka kwace;

6 podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo;

7 pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuucimo.

8 Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi iye;

9 podziwa kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siicitanso ufumu pa Iye.

10 Pakuti pakufa iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

11 Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.

12 Cifukwa cace musamalola ucimo ucite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zace:

13 ndipo musapereke ziwalo zanu kuucimo, zikhale zida za cosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo ataturuka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za cilungamo,

14 Pakuti ucimo sudzacita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a cisomo.

Ife ndife akapolo a Mulungu

15 Ndipo ciani tsono? Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri a lamulo, koma a cisomo? Msatero ai.

16 Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kucilungamo?

17 Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco;

18 ndipo pamene munamasulidwa kuucimo, munakhala akapolo a cilungamo,

19 Ndilankhula manenedwe a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa ndi a kusayeruzika kuti zicite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a cilungamo kuti zicite ciyeretso.

20 Pakuti pamene inu munali aka polo a ucimo, munali osatumikira cilungamo.

21 Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu izi ciri imfa.

22 Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuucimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli naco cobala canu cakufikira ciyeretso, ndi cimariziro cace moyo wosatha.

23 Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16