Aroma 9 BL92

Paulo alirira kusamvera kwa Israyeli

1 Ndinena zoona mwa Kristu, sindinama ai, cikumbu mtima canga cicita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,

2 kuti ndagwidwa ndi cisoni cacikuru ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.

3 Pakuti ndikadafunakuti ine ndekha nditembereredwe kundicotsa kwa Kristu cifukwa ca abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;

4 ndiwo Aisrayeli; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m'kacisi wa Mulungu, ndi malonjezo;

5 a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anacokera Kristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka ku nthawi zonse. Amen.

Ulamuliro wa Mulungu wakusankha ena

6 Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala cabe ai. Pakuti onse akucokera kwa a Israyeli siali Israyeli;

7 kapena cifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isake, mbeu yako idzaitanidwa.

8 Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yace.

9 Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana

10 Ndipo si cotero cokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isake;

11 pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo,

12 cotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.

13 Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.

14 Ndipo tsono tidzatani? Kodi ciripo cosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.

15 Pakuti anati ndi Mose, Ndidzacitira cifundo amene ndimcitira cifundo, ndipo ndidzakhala ndi cisoni kwa iye amene ndikhala naye cisoni.

16 Cotero sicifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene acitira cifundo.

17 Pakuti lembo linena kwa Farao, Cifukwa ca ici, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.

18 Cotero iye acitira cifundo amene iye afuna, ndipo amene iye afuna amuumitsamtima.

19 Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza cifuno cace?

20 Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi cinthu copangidwa cidzanena ndi amene anacipanga, U ndipangiranji ine cotero?

21 Kodi kapena woumba mbiya sakutha kucita zace padothi, kuumba ndi ncinci yomweyo cotengera cimodzi caulemu ndi cina camanyazi?

22 Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuonetsa mkwiyo wace, ndi kudziwitsa mph amvu yace, analekerera ndi cilekerero cambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera cionongeko?

23 ndi kuti iye akadziwitse ulemerero wace waukuru pa zotengera zacifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero,

24 ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu?

25 Monga atinso mwa Hoseya,Amene sanakhala anthu anga, ndidzawacha anthu anga;Ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.

26 1 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai,Pomwepo iwo adzachedwa ana a Mulungu wamoyo.

27 Ndipo Yesaya apfuula za Israyeli, kuti,2 Ungakhale unyinji wa ana a Israyeli ukhala monga mcenga wa kunyanja, 3 cotsalira ndico cidzapulumuka.

28 Pakuti Ambuye adzacita mau ace pa dziko lapansi, kuwatsiriza mwacidule.

29 Ndipo monga Yesaya anati kale,4 Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyira ife mbeu,Tikadakhala monga Sodoma, ndipo tikadafanana ndi Gomora.

30 Cifukwa cace tidzatani? 5 Kuti amitundu amene sanatsata cilungamo, anafikira cilungamo, ndico cilungamo ca cikhulupiriro;

31 6 koma Israyeli, potsata lamulo la cilungamo, sanafikira lamulolo.

32 Cifukwa canji? Cifukwa kuti sanacitsata ndi cikhulupiriro, koma monga ngati ndi nchito. 7 Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa;

33 monganso kwalembedwa, kuti,8 Onani, ndikhazika m'Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa;Ndipo 9 wakukhulupirira iye sadzacita manyazi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16