Macitidwe 28 BL92

Paulopa Melita

1 Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti cisumbuco cinachedwa Melita.

2 Ndipo akunja anaticitira zokoma zosacitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, cifukwa ca mvula inalinkugwa, ndi cifukwa ca cisanu.

3 Koma pamene Paulo adaola cisakata ca nkhuni, naciika pamoto, inaturukamo njoka, cifukwa ca kutenthaku, nilumadzanja lace.

4 Koma pamene akunjawo anaona ciromboco ciri lende pa dzanja lace, ananena wina ndi mnzace, Zoona munthuyu ndiye wambanda, angakhale anapulumuka m'nyanja, cilungamo sicimlola akhale ndi moyo.

5 Koma anakutumulira ciromboco kumoto, osamva kupweteka.

6 Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wace kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu.

7 Koma pafupt pamenepo panali minda, mwini wace ndiye mkulu cisumbuco, dzina lace Popliyo; amene anatilandira ife, naticereza okoma masiku atatu.

8 Ndipo kunatero kuti atate wace wa Popliyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namciritsa.

9 Ndipo patacitika ici, enanso a m'cisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, naciritsidwa;

10 amenenso anaticitira ulemu wambiri; ndipo pocoka ife anatiikira zotisowa.

Paulo afika ku Roma, nakhala wandende m'nyumba ya iye yekha zaka ziwiri

11 Ndipo itapita miyezi itatu tinayenda m'ngalawa ya ku Alesandriya, idagonera nyengo ya cisanu kucisumbuko, cizindikilo cace, Ana-a-mapasa.

12 Ndipo pamene tinakoceza ku Surakusa, tinatsotsako masiku atatu.

13 Ndipo pocokapo tinapaza ntifika ku Regio; ndipo litapita tsiku limodzi unayamba mwela, ndipo m'mawa mwace tinafika ku Potiyolo:

14 pamenepo tinakomana ndi abale, amene anatiumirira tikhale nao masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tinafika ku Roma.

15 Kucokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apiyo, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.

16 Ndipo pamene tinalowa m'Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikari womdikira iye.

17 Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinacita kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kucokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;

18 ndiwo, atandifunsafunsa ine anafuna kundimasula, popeza panalibe cifukwa ca kundiphera.

19 Koma pakukanapo Ayuda, ndinafulumidwa mtima kuturukira kwa Kaisara; si kunena kuti ndinali nako kanthu kakunenera mtundu wanga.

20 Cifukwa ca ici tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti cifukwa ca ciyembekezo ca Israyeli ndamangidwa ndi unyolo uwu.

21 Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandira akalata onena za inu ocokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.

22 Koma tifuna kumva mutiuze muganiza ciani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponse ponse.

23 Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza ku nyumba yace anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndikucitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zocokera m'cilamulo ca Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.

24 Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvera.

25 Koma popeza sanabvomerezana, anacoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,

26 ndi kuti,Pita kwa anthu awa, nuti,Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;Ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse;

27 Pakuti mtima wa anthu awa watupatu,Ndipo m'makutu mwao mmolemakumva,Ndipo masoao anawatseka;Kuti angaone ndi maso,Nangamve ndi makutu,Nangazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo Ine ndingawaciritse.

28 Potero, dziwani inu, kuti cipulumutso ici ca Mulungu citumidwa kwa amitundu; iwonsoadzamva. [

29 ]

30 Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m'nyumba yace yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye,

31 ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28