Macitidwe 17 BL92

Paulo ku Tesalonika ndi Bereya

1 Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.

2 Ndipo Paulo, monga amacita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,

3 natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.

4 Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akuru osati owerengeka.

5 Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa acabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nacititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwaturutsira kwa anthu.

6 Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akuru a mudzi, napfuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;

7 amene Yasoni walandira; ndipo onsewo acita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu.

8 Ndipo anabvuta anthu, ndi akuru a mudzi, pamene anamva zimenezi.

9 Ndipo pamene analandira cikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula.

10 Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Sila usiku kunka ku Bereya; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.

11 Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.

12 Ndipo ambiri a iwo anakhulupira; ndi akazi a Cihelene omveka, ndi amuna, osati owerengeka.

13 Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereyanso, anadza komwekonso, nautsa, nabvuta makamu.

14 Pomwepo abale anaturutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Sila ndi Timoteo anakhalabe komweko.

Paulo ku Atene

15 Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Sila ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi cangu conse, anacoka.

16 Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anabvutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano.

17 Cotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.

18 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikureya ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, ici ciani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zacilendo, cifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.

19 Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa ciphunzitso ici catsopano ucinena iwe?

20 Pakuti ufika nazo ku makutu athu zacilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani?

21 (Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osacita kanthu kena koma kunena kapena kumva catsopano.)

22 Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati,Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.

23 Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Cimene mueipembedza osacidziwa, cimeneco ndicilalikira kwa inu.

24 Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba zakacisi zomangidwa ndi manja;

25 satumikidwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;

26 ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;

27 kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patari ndi yense wa ife;

28 pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuyimba anu ati, Pakuti ifenso tiri mbadwa zace.

29 Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, woloca ndi luso ndi zolingalira za anthu.

30 Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima;

31 cifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'cilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse citsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.

32 Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za cimeneci.

33 Conco Paulo anaturuka pakati pao.

34 Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupira; mwa iwonso munali Dionisiyo Mareopagi, ndi mkazi dzina lace Damarisi, ndi ena pamodzi nao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28