Macitidwe 7 BL92

1 Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi?

2 Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harana;

3 nati kwa iye, Turuka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe.

4 Pamenepo anaturuka m'dziko la Akaldayo namanga m'Harana: ndipo, kucokera kumeneko, atamwalira atate wace, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;

5 ndipo sanampatsa colowa cace m'menemo, ngakhale popondapo phazi lace iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lace, ndi la mbeu yace yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.

6 Koma Mulungu analankhula cotero, kuti mbeu yace idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawacititsa ukapolo, nadzawacitira coipa, zaka mazana anai.

7 Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzaturuka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.

8 Ndipo anaiupatsa iye cipangano ca mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lacisanu ndi citatu; ndi Isake anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.

9 Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Aigupto; ndipo Mulungu anali naye,

10 namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.

11 Koma inadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi cisautso cacikuru; ndipo sanapeza cakudya makolo athu.

12 Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Aigupto, anatuma makolo athu ulendo woyamba,

13 Ndipo pa ulendo waciwiri Y osefe anazindikirika ndi abale ace; ndipo pfuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.

14 Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wace, ndi a banja lace lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.

15 Ndipo Yakobo anatsikira ku Aigupto; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;

16 ndipo anawanyamula kupita nao ku Sukemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wace wa ndalama kwa ana a Emori m'Sukemu.

17 Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nacuruka m'Aigupto,

18 kufikira inauka mfumu yina pa Aigupto, imene siinamdziwa Yosefe.

19 Imeneyo inacenjerera pfuko lathu, niwacitira coipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.

20 Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wace:

21 ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wace.

22 Ndipo Moseanaphunzira nzeru zonse za Aaigupto; nali wamphamvu m'mau ace ndi m'nchito zace.

23 Koma pamene zaka zace zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwace kuzonda abale ace ana a Israyeli,

24 Ndipo pakuona wina woti alikumcitira cotpa, iye anamcinjiriza, nambwezera cilango wozunzayo, nakantha M-aigupto.

25 Ndipo anayesa kuti abale ace akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa cipulumutso mwa dzanja lace; koma sanazindikira.

26 Ndipo m'mawa mwace anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; mucitirana coipa bwanji?

27 koma iye wakumcitira mnzace coipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira?

28 1 Kodi ufuna kundipha ine, monga muja unapha M-aigupto dzulo?

29 2 Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midyani; kumeneko anabala ana amuna awiri.

30 Ndipo 3 zitapita zaka makumi anai, anamuonekera mngelo m'cipululu ca Sina, m'lawi la mota wa m'citsamba.

31 4 Koma Mose pakuona, anazizwa pa coonekaco; ndipo pakuyandikira iye kukaona, kunadza mau a Ambuye,

32 5 akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isake, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako.

33 6 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Masula nsapato ku mapazi ako; pakuti pa malo amene upondapo mpopatulika.

34 7 Kuona ndaona coipidwa naco anthu anga ali m'Aigupto, ndipo a amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano tiye kuno, ndikutume ku Aigupto

35 Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkuru ndi woweruza? ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkuru, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pacitsamba.

36 Ameneyo anawatsogolera, naturuka nao 8 atacita zozizwa ndi zizindikilo m'Aigupto, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'cipululu zaka makumi anai.

37 Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israyeli, 9 Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.

38 10 Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'cipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sina, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;

39 amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha acoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Aigupto,

40 11 nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogoleraife; pakuti Mose uja, amene anatiturutsa m'Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.

41 Ndipo 12 anapanga mwana wa ng'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi nchito za manja ao.

42 Koma 13 Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku laaneneri,14 Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembeZaka makumi anai m'cipululu, nyumba ya Israyeli inu?

43 15 Ndipo munatenga cihema ca Moloki,Ndi nyenyezi ya mulungu Refani,Zithunzizo mudazipanga kuzilambira;Ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwace mwa Babulo.

44 Cihema ca umboni cinali ndi makolo athu m'cipululu, monga adalamula iye wakulankhula ndi Mose, 16 acipange ici monga mwa cithunzico adaciona.

45 17 Cimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa naco ndi Y oswa polandira iwo zao za amitundu, 18 amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davine;

46 amene anapeza cisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalama Mulungu wa Yakobo.

47 Kama 19 Solomo anammangira nyumba.

48 Komatu 20 Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,

49 21 Thambo la kumwamba ndilo mpando wacifumu wanga,Ndi dziko lapansi copondapo mapazi anga:Mudzandimangira nyumba yotani? ati Ambuye;Kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

50 Silinapanga dzanja langa zinthu izi zonse kodi?

51 22 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.

52 23 ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudzakwace kwa Wolungamayo; wa iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;

53 inu amene munalandira cilamulo 24 monga cidaikidwa ndi angelo, ndipo simunacisunga.

54 Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.

55 Koma iye, 25 pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,

56 nati, Taonani, 26 ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.

57 Koma anapfuula ndi mau akuru, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;

58 ndipo 27 anamtaya kunja kwa mudzi, namponya miyala; ndipo 28 mbonizo zinaika zobvala zao pa mapazi a mnyamata dzina lace Saulo.

59 Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, 29 Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.

60 Ndipo m'mene anagwada pansi, anapfuula ndi mau akuru, 30 Ambuye, musawaikire iwo cimo ili. Ndipo m'mene adanena ici, anagona tulo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28