Macitidwe 23 BL92

1 Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akuru anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi cikumbu mtima cokoma conse kufikira lero lomwe.

2 Ndipo mkulu wa ansembe Hananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pace.

3 Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa cilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga cilamulo?

4 Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?

5 Ndipo Paulo anati, Sindinadziwa, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera coipa mkulu wa anthu ako.

6 Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anapfuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa ciyembekezo ndi kuuka kwa akufa.

7 Ndipo pamene adatero, kunakhala cilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana.

8 Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi abvomereza ponse pawiri.

9 Ndipo cidauka cipolowe cacikuru; ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza coipa ciri conse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo: walankhula naye?

10 Ndipo pamene padauka cipolowe cacikuru, kapitao wamkuru anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikari atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga,

11 Ndipo usiku wace Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandicitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundicitira umboni ku Roma.

Ayuda apangana ciwembu ca kupha Paulo. Apulumukira ku Kaisareya

12 Ndipo kutaca, Ayuda anapangana ciwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;

13 ndipo iwo amene adacita cilumbiro ici anali oposa makumi anai.

14 Amenewo anadza kwa ansembe akulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo.

15 Potero tsopano inu ndi bwalo la akuru muzindikiritse kapitao wamkuru kuti atsikenaye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.

16 Koma mwana wa mlongo wace wa Paulo anamva za cifwamba cao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo.

17 Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkuru; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.

18 Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkuru, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.

19 Ndipo kapitao wamkuru anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Ciani ici uli naco kundifotokozera?

20 Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa ku bwalo la mirandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.

21 Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kud sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.

22 Pamenepo ndipo kapitao wamkuru anauza mnyamatayo apite, namlamulira kuti, Usauze munthu yense kuti wandizindikiritsa izi.

23 Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikari mazana awiri, apite kufikira Kaisareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, acoke ora lacitatu la usiku;

24 ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felike kazembeyo.

25 Ndipo analembera kalata wakuti:

26 Klaudiyo Lusiya kwa kazembe womveketsa Felike, ndikulankhulani.

27 Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikari, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.

28 Ndipo pofuna kuzindikira cifukwa cakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye ku bwalo la akuru ao.

29 Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a cilamulo cao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.

30 Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali ciwembu ca pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.

31 Pamenepo ndipo asilikari, monga adawalamulira, anatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri.

32 Koma m'mawa mwace anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga;

33 iwowo, m'mene anafika ku Kaisareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.

34 Ndipo m'mene adawerenga anafunsa acokera m'dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Kilikiya,

35 anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba yamlandu ya Herode.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28