Macitidwe 11 BL92

Petro adziwerengera pamaso pa Mpingo kuti anabatiza Komeliyo

1 Koma atumwi ndi abale akukhala m'Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.

2 Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo a kumdulidwe anatsutsana naye,

3 nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao.

4 Koma Petro anayamba kuwafotokozera cilongosolere, nanena,

5 Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, cotengera cirikutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pali ine;

6 cimeneco ndidacipenyetsetsa ndinacilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga.

7 Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye.

8 Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse.

9 Koma mau anayankha nthawi yaciwiri oturuka m'mwamba, Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera cinthu wamba.

10 Ndipo ici cinacitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.

11 Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ocokera ku Kaisareya.

12 Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo;

13 ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yace, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro;

14 amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse.

15 Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.

16 Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.

17 Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Kristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?

18 Ndipo pamene anamva izi, anakhala du, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, a Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.

Uthenga Wabwino ulalikidwa kwa amitundu a ku Antiokeya

19 Pamenepo iwotu, akubalalika cifukwa ca cisautsoco cidadza pa Stefano, anafikira ku Foinike, ndi Kupro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.

20 Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kupro, ndi Kurene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Ahelene, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.

21 Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupira unatembenukira kwa Ambuye.

22 Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala m'Yerusalemu; ndipo anatuma Bamaba apite kufikira ku Antiokeya;

23 ameneyo, m'mene anafika, naona cisomo ca Mulungu, anakondwa; ndipo anawandandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;

24 cifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi cikhulupiriro: ndipo khamu lalikuru lidaonjezeka kwa Ambuye.

25 Ndipo anaturuka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo;

26 ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti caka conse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kuchedwa Akristu ku Antiokeya.

27 Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya.

28 Ndipo anyanamuka mmodzi wa iwo, dzina lace Agabo, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudiyo.

29 Ndipo akuphunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m'Yudeya;

30 iconso anacita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Bamaba ndi Saulo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28