Macitidwe 14 BL92

Uthenga Wabwino ulalikidwa ku Ikoniyo, Lustra, ndi Derbe

1 Ndipo kunali pa Ikoniyo kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikuru la Ayuda ndi Ahelene anakhulupira.

2 Koma Ayuda osamvefa anautsa mitima ya Ahelene kuti aipse abale athu.

3 Cifukwa cace anakhala nthawi yaikuru nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anacitira umboni mau a cisomo cace, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zicitidwe ndi manja ao.

4 Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena analindi Ayuda, komaena anali ndi atumwi.

5 Ndipo pamene panakhala cigumukiro ca Ahelene ndi ca Ayuda ndi akuru ao, ca kuwacitira cipongwe ndi kuwaponya miyala,

6 iwo anamva, nathawira ku midzi ya Lukaoniya, Lustra ndi Derbe, ndi dziko lozungulirapo:

7 kumeneko ndiko Uthenga Wabwino.

8 Ndipo pa Lustra panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwace, wopunduka cibadwire, amene sanayenda nthawi zonse.

9 Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi cikhulupiriro colandira naco moyo,

10 anati ndi mau akuru, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda.

11 Pamene makamu anaona cimene anacita Paulo, anakweza mau ao, nati m'cinenero ca Lukaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.

12 Ndipo anamucha Bamaba, Zeu; ndi Paulo, Herme, cifukwa anali wotsogola kunena.

13 Koma wansembe wa Zeu wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.

14 Pamene anamva atumwi Paulo ndi Bamaba, anang'amba zopfunda zao, natumphira m'khamu,

15 napfuula Dati, Anthuni, bwanji mucita zimenezi? ifenso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zacabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse ziri momwemo:

16 m'mibadwo, yakale iye adaleka mitundu yonse iyende m'njira mwao.

17 Koma sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anacita zabwino, nakupatsani inu zocokera kumwamba mvulaodi nyengoza zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi cakudya ndicikondwero.

18 Pakunena izo, anabvutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo.

19 Ndipo anafika kumeneko Ayuda kucokera ku Antiokeya ndi Ikoniyo; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulomiyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa.

20 Koma pamene, anamzinga akuphunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwace anaturuka ndi Bamaba kunka, ku Derbe.

21 Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri akuphunzira, anabwera ku Lustra ndi Ikoniyo ndi Antiokeya,

22 nalimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandauliraiwo kuti akhalebe m'cikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

23 Ndipo pamene anawaikira akuru mosankha mu Mpingo Mpingo, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, anaikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.

24 Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfuliya.

25 Ndipo atalankhula mau m'Perge, anatsikira ku Ataliya;

26 komweko anacoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku cisomo ca Mulungu ku Ilchito imene adaimarizayo,

27 Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anacita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la cikhulupiriro.

28 Ndipo anakhala pamenepo ndi akuphunzira nthawi yaikuru.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28