Macitidwe 25 BL92

Paulo pa bwalo la miranda la Festo. Anena akaturukira kwa Kaisara

1 Pamenepo Festo m'mene analowa dziko lace, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka ku Yerusalemu kucokera ku Kaisareya.

2 Ndipo ansembe akulu ndi akulu a Ayuda ananenera Paulo kwa iye; ndipo iwo anamdandaulira,

3 nampempha kuti mlandu wace wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amcitira cifwamba kuti amuphe panjira.

4 Pamenepo Festo anayankha, kuti Paulo asungike ku Kaisareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posacedwa.

5 Cifukwa cace, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye.

6 Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikiraku Kaisareya; ndipo m'mawa mwace anakhala pa mpando waciweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.

7 Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikuru, zimene sanakhoza kuzitsimikiza;

8 koma Paulo podzikanira ananena, Sindinacimwa kanthu kapena pacilamulo, kapena paKacisi, kapena pa Kaisara.

9 Kama Festo pofuna kuyesedwa wacisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?

10 Koma Paulo anati, ndirikuimirira pa mpando waciweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawacitira-kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.

11 Pamenepo ngati ndiri wocita zoipa, ngati ndacita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zacabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditurukira kwa Kaisara.

12 Pamenepo Festo, atakamba ndi aphungu ace, anayankha, Wanena, Ndirurukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.

Paulo adzinenera kwa Agripa

13 Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Bemike anafika ku Kaisareya, nalankhula Festo.

14 Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Festo anafotokozera mfumuyo mlandu wace wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felike,

15 amene ansembe akulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndiri ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wace.

16 Koma ndinawayankha, kuti macitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa comneneraco.

17 Potero, pamene adasonkhana pano, sindinacedwa, koma m'mawa mwace ndinakhala pa mpando waciweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.

18 Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamchulira konse cifukwa ca zoipa zonga ndinazilingirira ine;

19 koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a cipembedzero ca iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.

20 Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndinamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za izi.

21 Koma pakunena Paulo ndi kuti, asungidwe, akaturukire kwa Augusto, ndinaweruza asungidwe iye kufikira ndikamtumiza kwa Kaisara.

22 Ndipo Agripa anati kwa Festo, Ndifuna nanenso ndimve munthuyo. Anati, Mawa mudzamva iye.

23 M'mawa mwace tsono, atafika Agripa ndi Bemike ndi cifumu cacikuru, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao akuru, ndi amuna omveka a mudziwo, ndipo pakulamulira Festo, anadza naye Paulo.

24 Ndipo Festo anati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kupfuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo.

25 Koma ndinapeza ine kuti sanacita kanthu, koyenera imfa iye; ndipo popeza, iye yekha anati akaturukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.

26 Koma ndiribe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Cifukwa cace ndamturutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.

27 Pakuti cindionekera copanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosachulanso zifukwa zoti amneneze.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28