Macitidwe 27 BL92

Amtumiza Paulo ku Roma. Tsoka panyanja

1 Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lace Yuliyo, wa gulu la Augusto.

2 Ndipo m'mene tidalowam'ngalawa ya ku Adramutiyo ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, dnakankha, ndipo Aristarko Mmakedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.

3 Ndipo m'mawa mwace tinangokoceza ku Sidoni; ndipo Yuliyo anacitira Paulo mwacikondi, namlola apite kwa abwenzi ace amcereze.

4 Ndipo pokankhanso pamenepo, tinapita kutseri kwa Kupro, popeza mphepo inaomba mokomana nafe.

5 Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwace kwa Kilikiya ndi Pamfiliya, tinafika ku Mura wa Lukiya.

6 Ndipo kenturiyo anapezako ngalawa ya ku Alesandriya, irikupita ku Italiya, ndipo anatilongamo.

7 Ndipo m'mene tidapita pang'ono pang'ono masiku ambiri, ndi kufika mobvutika pandunji pa Knido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinai pita m'tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone;

8 ndipo popaza-pazapo mobvutika, tinafika ku malo ena dzina lace Pokoceza Pokoma; pafupi pamenepo panali mudzi wa Laseya.

9 Ndipo Itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsya ulendowo, popezanso nyengo ya kusala cakudya idapita kale, Paulo anawacenjeza,

10 nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu.

11 Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.

12 Ndipo popezadooko silinakoma kugonapo nyengo yacisanu, unyinji unacita uphungu ndi kutiamasule nacokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Foinika, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwela.

13 Ndipo poomba pang'ono mwela, poyesa kuti anaona cofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.

14 Koma patapita pang'ono idaombetsa kucokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Eurokulo;

15 ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa.

16 Ndipo popita kutseri kwa cisumbu cacing'ono dzina lace Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma mobvutika;

17 ndipo m'mene adaukweza, anacita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Surti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.

18 Ndipo pobvutika kwakukuru ndi namondweyo, m'mawa mwace anayamba kutaya akatundu;

19 ndipo tsiku lacitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.

20 Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, ciyembekezo conse cakuti tipulumuke cidaticokera pomwepo.

21 Ndipo pamene atakhala nthawi yaikuru osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osacoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.

22 Koma tsopano ndikucenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.

23 Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndiri wace, amenenso ndimtumikira,

24 nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.

25 Cifukwa cace, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.

26 Koma tiyenera kutayika pa cisumbu cakuti.

27 Koma pofika usiku wakhumi ndi cinai, potengedwa ife kwina ndi kwina m'nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amarinyero anazindikira kuti analikuyandikira kumtunda;

28 ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu.

29 Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuce.

30 Ndipo m'mene amarinyero anafunakuthawa m'ngalawa, natsitsira bwato m'nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikuru,

31 Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikari, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka.

32 Pamenepo asilikari anadula zingwe za bwato, naligwetsa.

33 Ndipo popeza kulinkuca, Paulo anawacenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi cinai limene munalindira, ndi kusala cakudya, osalawa kanthu.

34 Momwemo ndikucenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa cipulumutsocanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pa mutu wa mmodzi wa inu.

35 Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m'mene adaunyema anayamba kudya.

36 Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga cakudya iwo omwe.

37 Ndipo life tonse tiri m'ngalawa ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi mmodzi.

38 Ndipo m'mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m'nyarija.

39 Ndipo kutaca sanazindikira dzikolo; koma anaona pali bondo la mcenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa.

40 Ndipo m'mene anataya anangula anawasiya m'nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikuru, analunjikitsa kumcenga.

41 Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikuru kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.

42 Ndipo uphungu wa asilikari udati awapheandende, angasambire, ndi kuthawa.

43 Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angacite ca uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziporiya m'nyanja, nafike pamtunda,

44 ndipo otsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m'ngalawa. Ndipo kudatero kuti lonse adapulumukira pamtunda.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28