Macitidwe 12 BL92

Herode azunza Eklesia; amupha Yakobo, naponya Petro kundende. Petro apulumuka m'ndende. Imfa ya Herode

1 Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Eklesia kuwacitira zoipa.

2 Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo a mbale wa Yohane.

3 Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda cotupitsa.

4 Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anai anai, amdikire iye; ndipo anafuna kumturutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha.

5 Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Eklesia anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.

6 Ndipo pamene Herode anati amturutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikari awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhalapakhomoanadikira ndende.

7 Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga, Ndipo maunyolo anagwa kucoka m'manja mwace.

8 Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'cuuno, numange nsapato zako. Nacita cotero. Ndipo ananena naye, Pfunda cobvala cako, nunelitsate ine.

9 Ndipo anaturuka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti ncoona cocitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.

10 Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi paciwiri, anadza ku citseko cacitsulo cakuyang'ana kumudzi; cimene cidawatsegukira cokha; ndipo anaturuka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamcokera.

11 Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wace nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku cilingiriro conse ca anthu a Israyeli.

12 Ndipo m'mene adalingirirapo, anadza ku nyumba ya Marlys amace wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera,

13 Ndipo m'mene anagogoda pa citseko ca pakhomo, linadza kudzabvomera buthu, dzina lace Roda.

14 Ndipo pozindikira mau ace a Petro, cifukwa ca kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.

15 Koma anati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo analimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo ananena, Ndiye mngelo wace.

16 Koma Petro anakhala cigogodere; ndipo m'mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa.

17 Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale cete, anawafotokozera umo, adamturutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi, Ndipo anaturuka napita kwina.

18 Koma kutaca, panali phokoso lalikuru mwa asilikari, Petro wamuka kuti.

19 Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kaisareya, nakhalabe kumeneko.

20 Koma Herode anaipidwa nao a ku Turo ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zocokera ku dziko la mfumu.

21 Ndipo tsiku lopangira Herode anabvala zobvala zacifumu, nakhala pa mpando wacifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.

22 Ndipo anthu osonkhanidwawo anapfuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai.

23 Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, cifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.

24 Koma mau a Mulungu anakula, nacurukitsa.

25 Ndipo Bamaba ndi Saulo anabwera kucokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28