Macitidwe 20 BL92

Paulo apitanso ku Makedoniya; ndi Helene, ndi Asiya

1 Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawacenjeza, analawirana nao, naturuka kunka ku Makedoniya.

2 Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawacenjeza, anadza ku Helene.

3 Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo a atampangira ciwembu Ayuda, pori iye apite ndi ngalawa ku Suriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Makedoniya.

4 Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatro mwana wa Puro, wa ku Bereya; ndipo Atesalonika, Aristarko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Derbe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tukiko ndi Trofimo.

5 Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Trowa.

6 Ndipo tinapita m'ngalawa kucokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda cotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Trowa; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.

7 Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere kufikira pakati pa usiku.

8 Ndipo munali nyali zambiri m'cipinda ca pamwamba m'mene tinasonkhanamo.

9 Ndipo mnyamata dzina lace Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikuru; ndipo pakukhala cifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja paciwiri, ndipo anamtola wakufa.

10 Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musacite phokoso, pakuti moyo wace ulipo.

11 Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kuca, anacokapo,

12 Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukuru.

13 Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira comweco, koma anati ayenda pamtunda yekha.

14 Ndipo pamene anakomana ndi ife ku Aso, tinamlandira, ndipo tinafika ku Mitilene.

15 Ndipo m'mene tidacokerapo, m'mawa mwace tinafika pandunjipa Kiyo; ndi m'mawa mwace tinangokoceza ku Samo, ndi m'mawa mwace tinafika ku Mileto.

16 Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.

Mau a Paulo kwa akuru a ku Efeso

17 Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo.

18 Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo,Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,

19 wotumikira Ambuye ndi kudzicepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;

20 kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba m'nyumba,

21 ndi kucitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi cikhulupiriro colinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.

22 Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidza'ndigwera ine kumeneko;

23 koma kuti Mzimu Woyera andicitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

24 Komatu sindiuyesa kanthu moyo, wanga, kuti uli wa mtengo wace kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kucitira umboni Uthenga Wabwino wa cisomo ca Mulungu.

25 Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.

26 Cifukwa cace ndikucitirani umboni lero lomwe, kuti ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.

27 Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.

28 Tadzicenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.

29 Ndidziwa ine kuti, nditacoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;

30 ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.

31 Cifukwa cace dikirani, nimukumbukile kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kucenjeza yense wa inu ndi misozi.

32 Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a cisomo cace, cimene ciri ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu colowa mwa onse oyeretsedwa.

33 Sindinasirira siliva, kapena golidi, kapena cobvala ca munthu ali yense.

34 Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine.

35 M'zinthu zonse ndinakupatsani citsanzo, cakuti pogwiritsa nchito, koteromuyenerakuthandiza ofoka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

36 Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.

37 Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pace, nampsompsona,

38 nalira makamaka cifukwa ca mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yace. Ndipo anamperekeza iye kungalawa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28