Macitidwe 13 BL92

Ulendo woyamba wa Paulo. Mpingo wa ku Antiokeya utuma Paulo ndi Bamaba amuke kwa amitundu, Alalikira pa Kupro, Elima watsenga

1 Ndipo kunali aneneri ndi aphunzioo ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnaba, ndi Sumeoni, wonenedwa Nigeri, ndi Lukiya wa ku Kurene, Manayeni woleredwa pamodzi ndi Herode ciwangaco, ndi Saulo.

2 Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.

3 Pamenepo, m'mene adasala cakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.

4 Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Selukeya; ndipo pocokerapo anapita m'ngalawa ku Kupro.

5 Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.

6 Ndipo m'mene anapitirira cisumbu conse kufikira Pafo, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lace Baryesu;

7 ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnaba ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.

8 Koma Elima watsengayo (pakuti dzina lace litera posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupire.

9 Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye,

10 nati, Wodzala ndi cinyengo conse ndi cenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa cilungamo conse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?

11 Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye liri pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapeoya dzuwa nthawi, Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamoka oaf una wina womgwira dzanja.

12 Pamenepo kazembe, pakuona cocitikacoanakhulupira, nadabwa naco ciphunzitso ca Ambuye.

Mau a Paulo m'sunagoge wa Antiokeya wa m'Pisidiya

13 Ndipo atamasula kucokera ku Pafo a ulendo wace wa Paulo anadza ku Perge wa ku Pamfuliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu.

14 Koma iwowa, atapita pocokera ku Perge anafika ku Antiokeya wa m'Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.

15 Ndipo m'mene adatha kuwerenga cilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.

16 Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati,Amuna a Israyeli, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.

17 Mulungu wa anthu awa Israyeli anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Aigupto, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawaturutsa iwo m'menemo.

18 Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'cipululu.

19 Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri m'Kanani, anawapatsa colowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;

20 ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samueli mneneriyo.

21 Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa pfuko la Benjamini, zaka makumi anai.

22 Ndipo m'mene atamcotsa iye, anawautsira Davine akhale mfumu yao; amenenso anamcitira umboni, nati, Ndapeza Davine, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzacita cifuniro canga conse.

23 Wocokera mu mbeu yace Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israyeli Mpulumutsi, Yesu;

24 Yohane atalalikiratu, asanafike iye, ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israyeli.

25 Ndipo pakukwaniritsa njira yace Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ace.

26 Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a cipulumutso ici.

27 Pakuti iwo akukhala m'Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikira iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.

28 Ndipo ngakhale sanapeza cifukwa ca kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe.

29 Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda.

30 Koma Mulungu anamuukitsa iye kwa akufa;

31 ndipo 1 anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza iye pokwera ku Yerusalemu kucokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumcitira umboni tsopano kwa anthu.

32 Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa 2 lonjezano locitidwa kwa makolo;

33 kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salmo laciwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.

34 Ndipo kuti anamuukitsa iye kwa akufa, wosabweranso kueibvundi, anateropo, 3 Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davine.

35 Cifukwa anenanso m'Salmo lina, 4 Simudzapereka Woyera wanu aone cibvundi.

36 Pakutitu, Davine, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwace mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ace, naona cibvundi;

37 koma iye amene Mulungu anamuukitsa sanaona cibvundi.

38 Potero padziwike ndi inu amuna abale, 5 kuti mwa iye cilalikidwa kwa inu cikhululukiro ca macimo;

39 ndipo 6 mwa iye yense wokhulupira ayesedwa wolungama kumcotsera zonse zimene simunangathe kudzicotsera poyesedwa wolungama ndi cilamulo ca Mose.

40 Cifukwa cace penyerani, kuti cingadzere inu conenedwa ndi anenenwo:

41 7 Taona ni, opeputsa inu, zizwani, kanganukani;Kuti ndigwiritsa nchito Ine masikuanu,Nchito imene simudzaikhulupira wina akakuuzani.

42 Ndipo pakuturuka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.

43 Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata. Paulo ndi Bamaba; amene, polankhula nao, 8 anawaumiriza akhale m'cisomo ca Ambuye.

44 Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mau a Mulungu.

45 Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nacita mwano.

46 Ndipo Paulo ndi Bamaba analimbika mtima ponena, nati, 9 Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. 10 Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.

47 Pakuti kotero anatilamulira Ambuye ndi kuti,11 Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu,Kuti udzakhala iwe cipulumutso kufikira malekezero a dziko.

48 Ndipo pakumva ici amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupira onse amene anaikidwiratu ku moyo wosatha.

49 Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m'dziko lonse.

50 Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, 12 nawautsira cizunzo Paulo ndi Bamaba, ndipo ana wapitikitsaiwom'malire ao.

51 Koma iwo, 13 m'mene adawasansirapfumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikoniyo,

52 Ndipo 14 akuphunzira anadzazidwa ndi cimwemwe ndi Mzimu Woyera.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28