Macitidwe 21 BL92

Paulo atabwera, ku Yerusalemu amgwira m'Kacisi

1 Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Ko, ndi m'mawa mwace ku Rode, ndipo pocokerapo ku Patara;

2 ndipo m'mene tinapeza ngalawa Yakuoloka kunka ku Foinike, tinalowamo, ndi kupita nayo.

3 Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kupro, tinacisiya kulamanzere, ntinapita ku Suriya; ndipo tinakoceza ku Turo; pakuti pamenepo ngalawainafuna kutula akatundu ace.

4 Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masikuasanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.

5 Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidacoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana anatiperekeza kufikira kuturuka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mcenga wa kunyanja, tinapemphera,

6 ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.

7 Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wocokera ku Turo, tinafika ku Ptolemayi; ndipo m'mene tidalankhula abale, tinakhala nao tsiku limodzi.

8 Ndipo m'mawa mwace tinacoka, ntinafika ku Kaisareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.

9 Ndipo munthuyu anali nao ana akazi anai, anamwali, amene ananenera.

10 Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeya mneneri, dzina lace Agabo.

11 Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a m'Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.

12 Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu.

13 Pamenepo Paulo anayankha, Mucitanji, polira ndi kundiswera mtima? pakuti ndakonzeka Ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.

14 Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kucitidwe.

15 Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu.

16 Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kaisareya, natenganso wina Mnaso wa ku Kupro, wophunzira wakale, amene adzaticereza.

17 Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera.

18 Ndipo m'mawa mwace Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.

19 Ndipo atawalankhula iwo, anawafotokozera cimodzi cimodzi zimene Mulungu anacita kwa amitundu mwa utumiki wace.

20 Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupira; ndipo ali naco cangu onsewa, ca pa cilamulo;

21 ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a ku amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo.

22 Nciani tsono? adzamva ndithu kuti wafika.

23 Cifukwa cace ucite ici tikuuza iwe; tiri nao amuna anai amene anawinda;

24 amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kati amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzacabe, koma kuti iwe wekhaoso uyenda molunjika, nusunga cilamulo.

25 Kama kunena za amitundu adakhulupirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.

26 Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwace m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kacisi, nauza cimarizidwe ca masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.

27 Ndipo pamene masiku asanu, ndi awiri anati amarizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kacisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,

28 napfuula, Amuna a Israyeli, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi cilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Ahelene nalowa nao m'Kacisi, nadetsa malo ana oyera.

29 Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye kuKacisi.

30 Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumturutsa m'Kacisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.

31 Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkuru wa gululo kuti m'Yerusalemumonse muli pinngu-piringu,

32 Ndipo posacedwa iye anatenga asilikari ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkuru ndi asilikari, analeka kumpanda Paulo.

33 Pamenepo poyandikira kapitao wamkuru anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awir; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anacita ciani?

34 Koma wina anapfuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona cifukwa ca phokosolo analamulira amuke naye kulinga.

35 Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikari cifukwa ca kulimbalimba kwa khamulo;

36 pakuti unyinji wa anthu unatsata, nupfuula, Mcotse iye.

37 Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkuru, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Cihelene?

38 Si ndiwe M-aigupto uja kodi, unacita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kucipululu?

39 Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m'Kilikiya, mfulu ya mudzi womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.

40 Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala cete onse, analankhula nao m'cinenedwe ca Cihebri, nanena.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28