Macitidwe 8 BL92

Uthenga Wabwino pa Samariya. Simoni wanyanga

1 Ndipo Saulo analikubvomerezana nao pa imfa yace. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukuru pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi samariya, koma osati atumwi ai.

2 Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro akuru.

3 Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa m'nyumba m'nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.

4 Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.

5 Ndipo Filipo anatsikira ku mudzi wa ku Samarlya, nawalalikira iwo Kristu.

6 Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikilo zimene anazicita.

7 Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawaturukira, yopfuula ndi mau akuru; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anaciritsidwa.

8 Ndipo panakhala cimwemwe cacikuru m'mudzimo.

9 Koma panali munthu dzina lace Simoni amene adacita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkuru;

10 ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikuru.

11 Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikuru adawadabwitsa iwo ndi matsenga ace.

12 Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwinowa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.

13 Ndipo Simoni mwini wace anakhulupiranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikilo ndi mphamvu zazikuru zirikucitika, anadabwa.

14 Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;

15 amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:

16 pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwam'dzina la Ambuye Yesu.

17 Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

18 Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,

19 nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene ali yense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.

20 Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, cifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.

21 Ulibe gawo kapena colandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.

22 Cifukwa: cace lapa coipa calm ici, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe colingiriraca mtima wako.

23 Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya cosalungama.

24 Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.

25 Pamenepo iwo, atatha kucita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwerakunkaku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwi no ku midzi yambirl ya Asamariya.

Filipo ndi mdindo wa ku Aitiopiya

26 Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwela, kutsata njira yotsika kucokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya cipululu.

27 Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya, ndiye wakusunga cuma cace conse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;

28 ndipo analinkubwerera, nalikukhala pa gareta wace, nawerenga mneneri Yesaya.

29 Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike ku gareta uyu.

30 Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira cimene muwerenga?

31 Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.

32 Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo.Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa,Ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga,Kotero sanatsegula pakamwa pace:

33 M'kucepetsedwa kwace ciweruzo cace cinacotsedwa;Mbadwo wace adzaubukitsa ndani?Cifukwa wacotsedwa kudziko moyo wace.

34 Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ici za yani? za yekha, kapena za wina?

35 Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pace, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.

36 Ndipo monga anapita paniire pao, anadza ku madzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; cindiletsa ine ciani ndisabatizidwe? [

37 ]

38 Ndipo anamuuza kuti aimitse gareta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipoanambatiza iye.

39 Ndipo pamene anakwera kururuka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonanso, pakuti anapita njira yace wokondwera.

40 Koma Filipo anapezedwa ku Azotu; ndipo popitapitaanalalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kaisareya.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28