Macitidwe 24 BL92

Felike amva mlandu wa Paulo

1 Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Hananiya pamodzi ndi akuru ena, ndi wogwira moyo dzina lace Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.

2 Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena.Popeza tiri nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,

3 tizilandira ndi ciyamiko conse, monsemo ndi ponsepo, Felike womveka inu.

4 Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupempha, ni mutimvere mwacidule ndi cifatso canu.

5 Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;

6 amenenso anayesa kuipsa Kacisi; amene tamgwira;

8 kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi.

9 Ndipo Ayudanso anabvomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.

10 Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;

11 popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha cikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira;

12 ndipo sanandipeza m'Kacisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda.

13 Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano.

14 Koma ici ndibvomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupira zonse ziri monga mwa cilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;

15 ndi kukhala naco ciyembekezo ca kwa Mulungu cimene iwo okhanso acilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.

16 M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale naco nthawi zonse cikumbu mtima cosanditsutsa ca kwa Mulungu ndi kwa anthu.

17 Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zacifundo, ndi zopereka;

18 popereka izi anandipeza woyeretsedwa m'Kacisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; koma panali Ayuda ena a ku Asiya,

19 ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.

20 Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza cosalungama cotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akuru,

21 koma mau awa amodzi okha, amene ndinapfuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.

22 Koma Felike anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lusiya kapitao wamkuru akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.

23 Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ace kumtumikira.

24 Koma atapita masiku ena, anadza Felike ndi Drusila mkazi wace, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za cikhulupiriro ca Kristu Yesu.

25 Ndipo m'mene anamfotokozera za cilungamo, ndi cidziletso, ndi ciweruziro cirinkudza, Felike anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.

26 Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; cifukwa cacenso anamuitana iye kawiri kawiri, nakamba naye.

27 Koma zitapita zaka ziwiri Porkiyo Festo analowa m'malo a Felike; ndipo Felike pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28