Macitidwe 26 BL92

1 Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:

2 Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;

3 makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; cifukwa cace ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.

4 Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa cibwana canga, amene anakhala ciyambire mwa mtundu wanga m'Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse;

5 andidziwa ine ciyambire, ngati afuna kucitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa cipembedzero cathu.

6 Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa ciyembekezo ca lonjezano limene Mulungu analicita kwa makolo athu;

7 kunkira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Cifukwa ca ciyembekezo ici, Mfumu, andinenera Ayuda.

8 Muciyesa cinthu cosakhulupirika, cakuti Mulungu aukitsa akufa?

9 Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.

10 Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.

11 Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.

12 M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe akulu, dzuwa lamsana,

13 ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kocokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa, kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.

14 Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'cinenedwe ca Cihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? nkukubvuta kutsalima pacothwikira.

15 Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.

16 Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti cifukwa ca ici ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo we;

17 ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwa amitundu, amene Ine ndikutuma kwa iwo,

18 kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine.

19 Potero, Mfumu Agripa, sindinakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba;

20 komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kucita nchito zoyenera kutembenuka mtima.

21 Cifukwa ca izi Ayuda anandigwira m'Kacisi, nayesa kundipha.

22 Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwacitira umboni ang'ono ndi akuru, posanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananenazidzafika;

23 kuti Kristu akamve zowawa, kuti iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.

24 Koma pakudzikanira momwemo, Festo anati ndi mau akuru, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakucititsa misala.

25 Koma Paulo anati, Ndiribe misala, Festo womvekatu; koma nditurutsa mau a coonadi ndi odziletsa.

26 Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ici Sicinacitika m'tseri.

27 Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? ndidziwa kuti muwakhulupirira.

28 Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang'ono ufuna kundiyesera Mkristu.

29 Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndiri ine, osanena nsinga izi.

30 Ndipo ananyamuka mfumu, ndi kazembe, ndi Bemike, ndi iwo akukhala nao;

31 ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzace, nanena, Munthu uyu sanacita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.

32 Ndipo Agripa anati kwa Festo, Tikadakhoza kumasula munthuyu, wakadapanda kunena, Ndikaturukire kwa Kaisara.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28