Macitidwe 19 BL92

Ulendo wacitatu wa Paulo. Demetrio autsa phokoso

1 Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza akuphunzira ena;

2 ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupira? Ndipo anati, lai, sitinamva konsekuti Mzimu Woyera waperekedwa.

3 Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'ciani? Ndipo anai, Mu ubatizo wa Yohane.

4 Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire iye amene adzadza pambuyo pace, ndiye Yesu.

5 Pamene anamva ici, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.

6 Ndipo pamene Paulo anaika manja ace pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

7 Onsewo anali ngati amuna khumi ndi awiri.

8 Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.

9 Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawacokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Turano.

10 Ndipo anacita comweco zaka ziwiri; kotero kuti onseakukhala m'Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene.

11 Ndipo Mulungu anacita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo;

12 kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsaru zopukutira ndi za panchito, zocokera pathupi pace, ndipo nthenda zinawacokera, ndi mizimu yoipa inaturuka.

13 Koma Ayuda enanso oyendayenda, oturutsa ziwanda, anadziyesa kuchula pa iwo amene anali ndi mizimu yoipa dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.

14 Ndipo panali ana amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkuru wa ansembe amene anacita ici.

15 Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?

16 Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amarisece ndi olasidwa.

17 Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Yesu Iinakuzika.

18 Ndipo ambiri a iwo akukhulipirawo anadza, nabvomereza, nafotokoza macitidwe ao.

19 Ndipo ambiri a iwo akucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wace, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.

20 Cotero mau a Ambuye anacuruka mwamphamvu nalakika.

21 Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wace, atapita pa Makedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.

22 Pamene anatuma ku Makedoniya awiri a iwo anamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini anakhalabe nthawi m'Asiya.

23 Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.

24 Pakuti munthu wina dzina lace Demetriyo wosula siliva, amene anapanga tiakacisi tasiliva ta Artemi, anaonetsera amisiri phindu lambiri;

25 amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a nchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza cuma cathu.

26 Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:

27 ndipo tiopa ife kuti nchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti kacisi wa mlungu wamkazi Artemi adzayamba kuyesedwa wacabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wace, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.

28 Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, napfuula, nati, Wamkuru ndi Artemi wa ku Efeso,

29 Ndipo m'mudzi monse munacita piringu-piringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristarko, anthu a ku Makedoniya, alendo anzace a Paulo.

30 Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, akuphunzira ace sanamloleza.

31 Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ace, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye ku bwalo lakusewera.

32 Ndipo ena anapfuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa cifukwa cace ca kusonkhana.

33 Ndipo anaturutsa Alesandro m'khamumo, kumturutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.

34 Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akupfuula monga maora awiri, Wamkuru ndi Artemi wa Aefeso.

35 Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mudzi wa Aefeso ndiwo wosungira kacisi wa Artemi wamkuru, ndi fano Iidacokera kwa Zeu?

36 Popeza tsono izi sizikanika, muyenera inu kukhala cete, ndi kusacita kanthu kaliuma.

37 Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za m'kacisi, kapena ocitira mulungu wathu mwano.

38 Ngati tsono Demetriyo ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a mirandu alipo, ndi ziwanga ziripo; anenezane.

39 Koma ngati mufuna kanthu ka zinthu zina, kadzakonzeka m'msonkhano wolamulidwa.

40 Pakutinso palipo potiopsya kuti adzatineneza za cipolowe ca lero; popeza palibe cifukwa ca kufotokozera za cipiringu cimene.

41 Ndipo pamene ananena izi, anamasula msonkhano.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28