Macitidwe 15 BL92

Ku Yerusalemu atumwi ndi akuru aweruza za mdulidwe ndi malamulo a Mose

1 Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapandakudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.

2 Ndipo pamene Paulo ndi Bamaba anacitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Bamaba, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akuru kukanena za funsolo.

3 Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Foinike ndi Samariya, nafotokozera cisanduliko ca amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.

4 Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akuru, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anacita nao.

5 Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge cilamulo ca Mose.

6 Ndipo anasonkhana atumwi ndi akuru kuti anene za mlanduwo.

7 Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupire.

8 Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawacitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;

9 ndipo sanalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'cikhulupiriro.

10 Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la akuphunzira gori, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

11 Koma tikhulupira tidzapulumuka mwa cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, monga iwo omwe.

12 Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Bamaba ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anacita nao pa amitundu.

13 Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati,Abale, mverani ine:

14 Sumeoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lace.

15 Ndipo mau a aneneri abvomereza pamenepo; monga kunalembedwa,

16 Zikatha izo ndidzabwera, Ndidzamanganso cihema ca Davine, cimene cinagwa;Ndidzamanganso zopasuka zace,Ndipo ndidzaciimikanso:

17 Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye,Ndi amitundu onse amene dzina langa linachulidwa pa iwo,

18 Ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo ciyambire dzikolapansi.

19 Cifukwa cace ine ndiweruza, kuti tisabvute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,

20 koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.

21 Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m'midzi yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ace m'masunagoge masabata onse.

22 Pamenepo cinakomera atumwi ndi akuru ndi Eklesia yensekusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Bamaba; ndiwo Yuda wochedwa Barsaba, ndi Sila, akuru a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:

23 Atumwi ndi abale akuru kwa abale a mwa amitundu a m'Antiokeya, ndi Suriya, ndi Kilikiya, tikulankhulani:

24 Popeza tamva kuti ena amene anaturuka mwa ife anakubvutani ndi mau, nasoceretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira;

25 cinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Bamaba ndi Paulo,

26 anthu amene anapereka moyo wao cifukwa ca dzina la Yesu Kristu Ambuye wathu.

27 Tatumiza tsono Yuda ndi Sila, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo.

28 Pakuti cinakomer a Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu cothodwetsa cacikuru cina coposa izi zoyenerazi;

29 kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.

30 Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.

31 Pamene anawerenga, anakondwera cifukwa ca cisangalatso cace.

32 Ndipo Yuda ndi Sila, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.

33 Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza. [

34 ]

35 Koma Paulo ndi Bamaba anakhalabe m'Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.

Paulo ndi Bamaba alekana

36 Patapita masiku, Paulo anati kwa Bamaba, Tibwerenso, tizonde abale m'midzi yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.

37 Ndipo Bamaba anafuna kumtenga Yohane uja, wochedwa Marko.

38 Koma sikunamkomera Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nao kunchito.

39 Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzace; ndipo Bamaba anatenga Marko, nalowa n'ngalawa, nanka ku Kupro.

Ulendo waciwiri wa Paulo

40 Koma Paulo anasankha Sila, namuka, woikizidwa ndi abale ku cisomo ca Ambuye.

41 Ndipo iye anapita kupyola pa Suriya ndi Kilikiya, nakhazikitsa Mipingo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28