Macitidwe 22 BL92

Paulo acita codzikanira cace kwa anthu

1 Amuna, abale, ndi atate, mverani codzikanira canga tsopano, ca kwa inu.

2 Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'cinenedwe ca Cihebri, anaposa kukhala cete; ndipo anati:

3 ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Kilikiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliyeli, wolangizidwa monga mwa citsatidwe ceni ceni ca cilamulo ca makolo athu, ndipo ndinali wacangu, colinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;

4 ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.

5 Monganso mkulu wa ansembe andicitira umboni, ndi bwalo lonse la akuru; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.

6 Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukuru kocokera kumwamba.

7 Ndipo ndinagwapansitu, ndipondinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilonda-londeranii Ine?

8 Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa Ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.

9 Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamva mau akulankhula nane.

10 Ndipo ndinati, ndidzacita ciani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Taukavpita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzicite.

11 Ndipo popeza sindinapenya, cifukwa ca ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.

12 Ndipo munthu dzina lace Hananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa cilamulo, amene amcitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako,

13 anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.

14 Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe cifuniro cace, nuone Wolungamayo, numve mau oturuka m'kamwa mwace.

15 Ndipo udzamkhalira iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva.

16 Ndipo tsopano ucedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kucotsa macimo ako, nuitane pa dzina lace.

17 Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera m'Kacisi, ndinacita ngati kukomoka,

18 ndipo ndinamuona iye, nanena nane, Fulumira, turuka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.

19 Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu;

20 ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kubvomerezana nao, ndi kusunga Zoobvala za iwo amene anamupha iye.

21 Ndipo anati kwa ine, Pita; cifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.

22 Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Acoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

23 Ndipo pakupfuula iwo, ndi kutaya zobvala zao, ndi kuwaza pfumbi mumlengalenga,

24 kapitao wamkuru analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe cifukwa cace nciani kuti ampfuulira comweco.

25 Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodinkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wace wosamveka?

26 Ndipo pakumva ici kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkuru, namuuza, nanena, Nciani ici uti ucite? pakuti munthuyo ndiye Mroma.

27 Ndipo kapitao wamkuruyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde.

28 Ndipo kapitao wamkuru anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wace waukuru. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.

29 Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkurunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.

Paulo pa bwalo la akuru

30 Koma m'mawa mwace pofuna kuzindikira cifukwa cace ceni ceni cakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe akulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28