Macitidwe 2 BL92

Tsiku la Pentekoste

1 Ndipo pakufika tsiku la Penteskoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi.

2 Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ocokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.

3 Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha.

4 Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.

5 Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ocokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo.

6 Koma pocitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'cilankhulidwe cace ca iye yekha.

7 Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?

8 ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'cilankhulidwe cathu cimene tinabadwa naco?

9 Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya;

10 m'Frugiya, ndiponso m'Pamfuliya, m'Aigupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo ocokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka,

11 Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikuru za Mulungu.

12 Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzace, Kodi ici nciani?

13 koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero.

Codzikanira ca Petro

14 Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ace, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu m'Yerusalemu, ici cizindikirike kwa inu, ndi po cherani khutu mau anga.

15 Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi ora lacitatulokha la tsiku;

16 komatu ici ndi cimene cinanenedwa ndi mneneri Yoeli,

17 Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu,Ndidzathira ca Mzimu wansa pa thupi liri lonse,Ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera,Ndipo anyamata anu adzaona masomphenya,Ndi akulu anu adzalota maloto;

18 Ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awaNdidzathira ca Mzimu wanga; ndipo adzanenera.

19 Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba,Ndi zizindikilo pa dziko lapansi;Mwazi, ndi moto, ndi mpweya wautsi;

20 Dzuwa lidzasanduka mdima,Ndi mweziudzasanduka mwazi,Lisanadze tsiku la Ambuye,Lalikuru ndi loonekera;

21 Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina laAmbuye adzapulumutsidwa.

22 Amuna inu Aisrayeli, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wocokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndizimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikilo, zimene Mulungu anazicita mwa iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha;

23 ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampacika ndi kumupha ndi manja a anthu osayeruzika;

24 yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti iye agwidwe nayo.

25 Pakuti Davine anena za Iye,Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse;Cifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;

26 Mwa ici unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa;Ndipo thupi langanso lidzakhala m'ciyembekezo.

27 Pakuti simudzasiya moyo wanga ku Hade,Kapena simudzapereka Woyera wanu aone cibvunde,

28 Munandidziwitsa ine njira za moyo;Mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.

29 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davine, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ace ali ndi ife kufikira lero lino.

30 Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi Iumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa cipatso ca m'cuuno mwace adzakhazika wina pa mpando wacifumu wace;

31 iye pakuona ici kale, analankhula za kuuka kwa Kristu, kuti sanasiyidwa m'Hade, ndipo thupi lace silinaona cibvunde.

32 Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ici tiri mboni ife tonse.

33 Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja Lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ici, cimene inu mupenya nimumva.

34 Pakuti Davine sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha,Ambuye anati kwa Mbuye wanga,Khalani ku dzanja lamanja langa,

35 Kufikira ndikaike adani ako copondapo mapazi ako.

36 Pamenepo lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampacika.

Otembenuka mtima oyamba

37 Koma pamene anamva ici, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzacita ciani, amuna inu, abale?

38 Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

39 Pakuti lonjezano 1 liri kwa inu, ndi kwa ana anu, 2 ndi kwa onse akutali, 3 onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

40 Ndipo ndi mau ena ambiri anacita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.

41 Pamenepo iwo amene analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

42 Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

43 Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo 5 zozizwa ndi zizindikilo zambiri zinacitika ndi atumwi.

44 Ndipo onse akukhulupira anali pamodzi, 6 nakhala nazo zonse zodyerana.

45 Ndipo zimene anali nazo, ndi cuma cao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.

46 Ndipo tsiku ndi tsiku 7 anali cikhalire ndi mtima umodzi m'Kacisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira cakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;

47 nalemekeza Mulungu, 8 ndi kukhala naco cisomo ndi anthu onse. Ndipo 9 Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28