Macitidwe 16 BL92

1 Ndipo anafikanso ku Derbe ndi Lustra; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lace Timoteo, amace ndiye Myuda wokhulupira; koma atate wace ndiye Mhelene.

2 Ameneyo anamcitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.

3 Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, cifukwa ca Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wace anali Mhelene.

4 Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akuru a pa Yerusalemu.

5 Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao tsiku ndi tsiku.

6 Ndipo anapita pa dziko la Frugiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya; pamene anafika kundunji kwa Musiya,

7 anayesa kunka ku Bituniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;

8 ndipo pamene anapita pambali pa Musiya, anatsikira ku Trowa.

Masomphenya a ku Trowa. Paulo aoloka nalalikira ku Filipi. Za Lidiya wogulitsa cibakuwa. Mdindo wa ku Filipi

9 Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Makedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.

10 Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kuturukirakunka ku Makedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.

11 Cotero tinacokera ku Trowa m'ngalawa, m'mene tinalunjikitsa ku Samotrake, ndipo m'mawa mwace ku Neapoli;

12 pocokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Makedoniya, waukuru wa m'dzikomo, wa miraga ya Roma; ndipojidagona momwemo masiku ena.

13 Tsiku la Sabata tinaturuka kumudzi kunka ku mbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana,

14 Ndipo anatimva mkazi wina dzina lace Lidiya, wakugulitsa cibakuwa, wa ku mudzi wa Tiyatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wace Ambuye anatsegula, kuti amvere zimene anazinena Paulo.

15 Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pace anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.

16 Ndipo panali, pamene tinalinkunka kukapemphera, anakomana ndi ife namwali wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ace zambiri pakubwebweta pace.

17 Ameneyo anatsata Paulo ndi ite, napfuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba amene akulalikirani inu njira ya cipulumutso.

18 Ndipo anacita cotero masiku ambiri. Koma Paulo anabvutika mtima ndithu, naceuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Kristu, turuka mwa iye. Ndipo unaturuka nthawi yomweyo.

19 Koma pamene ambuye ace anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akuru,

20 ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa abvuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda,

21 ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuicita, ndife Aroma.

22 Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira maraya ao; nalamulira kuti awakwapule.

23 Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.

24 Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'cipinda ca m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo.

25 Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Sila analinkupemphera, nayimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;

26 ndipo mwadzidzidzi panali cibvomezi cacikuru, cotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.

27 Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lace, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa.

28 Koma Paulo anapfuula ndi mau akuru, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tiri muno.

29 Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m'kati, alinkunthunthunrlra ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Sila,

30 nawaturutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndicitenji kuti ndipulumuke?

31 Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.

32 Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pace.

33 Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pace.

34 Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwace, nawakhazikira cakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pace, atakhulupirira Mulungu.

35 Kutaca, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.

36 Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu turukani, mukani mumtendere.

37 Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ire pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ire amene tiri Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutiturutsira ire m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atiturutse.

38 Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma.

39 Ndipo anadza nawapembedza; ndipo pamene anawaturutsa, anawapempha kuti acoke pamudzi.

40 Ndipo anaturukam'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidiya: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28