Macitidwe 1 BL92

Yesu akwera kunka Kumwamba

1 TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzicita ndi kuziphunzitsa,

2 kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;

3 kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zace, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumuwa Mulungu;

4 ndipo e posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asacoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;

5 pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.

6 Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?

7 Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha.

8 Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.

9 Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao.

10 Ndipo pakukhala iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala zoyera anaimirira pambali pao;

11 amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

12 Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kucokera ku phiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.

13 Ndipo pamene adalowa, anakwera ku cipinda ca pamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andreya, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeyu ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyu, ndi Simoni Zelote, ndi Yuda mwana wa Yakobo.

14 Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Mariya, amace wa Yesu, ndi abale ace omwe.

15 Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),

16 Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davine za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.

17 Cifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lace la utumiki uwu.

18 (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphoto ya cosalungama; ndipo anagwa camutu, naphulika pakati, ndi matumbo ace onse anakhuthuka;

19 ndipo cinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m'manenedwe ao kadzikoka kanachedwa Akeldama, ndiko, kadziko ka mwazi.)

20 Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalmo,Pogonera pace pakhale bwinja,Ndipo pasakhale munthu wogonapo;Ndipo uyang'aniro wace autenge wina.

21 Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa naturuka mwa ife,

22 kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwace pamodzi ndi ife.

23 Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wochedwa Barsaba, amene anachedwanso Yusto, ndi Matiya.

24 Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikiramitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,

25 alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kucokera komwe Yudase anapatukira, kuti apite ku malo a iye yekha.

26 Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiya; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28