Yohane 21 BL92

Yesu awaonekera ku nyanja ya Tiberiva

1 Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa akuphunzira ace ku nyanja ya Tiberiya. Koma anadzionetsera cotere.

2 Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wochedwa Didimo, ndi Natanayeli wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedayo, ndi awiri ena a akuphunzira ace.

3 Simoni Petro ananena nao, ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anaturuka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu.

4 Koma pakuyamba kuca, Yesu anaimirira pam bali pa nyanja, komatu akuphunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu.

5 Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha iye, lai.

6 Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka ku mbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza, Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka cifukwa ca kucuruka nsomba.

7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadzibveka maraya a pathupi, pakuti anali wamarisece, nadziponya yekha m'nyanja.

8 Koma akuphunzira ena anadza m'kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo.

9 Ndipo pamene anaturukira pamtunda, anapenya moto wamakara pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate.

10 Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano,

11 Cifukwa cace Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda Iodzala ndi nsomba zazikuru, zana limodzi, ndi makumiasanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinacuruka kotere, kokha silinang'ambika.

12 Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa akuphunzira anatha kumfunsa iye, Ndinu yani? podziwa kuti ndiye Ambuye.

13 Yesu anadza natenga mkate napatsa Iwo, momwemonso nsomba.

14 Imeneyo ndi nthawi yacitatu yakudzionetsera Yesu kwa akuphunzira ace, m'mene atauka kwa akufa.

15 Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa ana a nkhosa anga.

16 Ananena nayenso kaciwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.

17 Ananena: naye kacitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva cisoni kuti anati kwa iye kacitatu, Kodi undikonda Ine? ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.

18 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'cuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzaturutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.

19 Koma ici ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ici, anati kwa iye, nditsate Ine,

20 Petro, m'mene anaceuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pacifuwa pace pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?

21 Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu?

22 Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli ciani ndi iwe? unditsate Ine iwe.

23 Cifukwa cace mau awa anaturuka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli ciani ndi iwe?

24 Yemweyu ndiye wophunzira wakucita umboniza izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wace ndi woona.

25 Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21