Yohane 4 BL92

Mkazi wa ku Samariya

1 Cifukwa cace pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane

2 (angakhale Yesu sanabatiza yekha koma ophunzira ace),

3 anacokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya.

4 Ndipo anayenerakupita pakati pa Samariya.

5 Cifukwa cace anadza ku mudzi wa Samariya, dzina lace Sukari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wace Yosefe;

6 ndipo pamenepo panali citsime ca Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wace, motero anakhala pacitsime,

7 Kunali ngati ora lacisanu ndi cimodzi. Kunadza mkazi woturuka m'Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.

8 Pakuti ophunzira ace adacoka kunka kumudzi kuti akagule cakudya.

9 Pamenepo mkazi wa m'Samariya ananena ndi iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya),

10 Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.

11 Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe cotungira madzi, ndi citsime ciri cakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo?

12 kodi muli wamkuru ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife citsimeci, namwamo iye yekha, ndi ana ace, ndi zoweta zace?

13 Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso Iudzu;

14 koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.

15 Mkaziyo ananena kwa iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga.

16 Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.

17 Mkazi anayankha nati kwa iye, Ndiribe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe;

18 pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala nave tsopano sali mwamuna wako; ici wanena zoona.

19 Mkazi ananena ndi iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri.

20 Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo ozenera kulambiramo anthu.

21 Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu.

22 Inu mulambira cimene simucidziwa; ife tilambira cimene ticidziwa; pakuti cipulumutso cicokera kwa Ayuda.

23 Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'coonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ace.

24 Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'coonadi.

25 Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wochedwa Kristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.

26 Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.

27 Ndipo pamenepo anadza ophunzira ace; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna ciani? kapena, mulankhula naye ciani?

28 Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wace, namuka kumudzi, nanena ndi anthu,

29 Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu ziri zonse ndinazicita: ameneyu sali Kristu nanga?

30 Anaturuka iwo m'mudzi ndipo analinkudza kwa iye.

Za masika ndi anchito

31 Pa mphindikati iyi ophunzira ace anampempha iye, ndi kunena, Rabi, idyani.

32 Koma iye anati kwa iwo, Ine ndiri naco cakudya cimene inu simucidziwa.

33 Cifukwa cace ophunzira ananena wina ndi mnzace, Kodi pali wina anamtengera iye kanthu kakudya?

34 Yesu ananena nao, Cakudya canga ndico kuti ndicite cifuniro ca iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza nchito yace.

35 Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.

36 Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira cobala ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.

37 Pakuti m'menemo conenaco ciri coona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso.

38 Ine ndinatuma inu kukamweta cimene simunagwirirapo nchito: ena anagwira nchito, ndipo inu mwalowa nchito yao.

Yesu ndi Asamariya

39 Ndipo m'mudzi mula anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira iye cifukwa ca mau a mkazi, wocita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu ziri zonse ndinazicita.

40 Cifukwa cace pamene Asamariya anadza kwa iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.

41 Ndipo ambiri oposa anakhulupira cifukwa ca mau ace:

42 ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupira cifukwa ca kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.

Yesu aciritsa mwana wa Mkuru

43 Koma atapita masiku awiriwo anacoka komweko kunka ku Galileya.

44 Pakuti Yesu mwini anacita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao.

45 Cifukwa cace pamene anadza ku Galileya, Agalileva anamlandira iye, atakaona zonse zimene anazicita m'Yerusalemu paphwando; pakuti iwonso ananka kuphwando.

46 Cifukwa cace Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunalimkulu wina wa mfumu, mwana wace anadwala m'Kapernao.

47 Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wacokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa iye, nampempha kuti atsike kukaciritsa mwana wace; pakuti anali pafupi imfa.

48 Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikilo ndi zozizwa, simudzakhulupira.

49 Mkuluyo ananena kwa iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga.

50 Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo, Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka.

51 Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ace anakomana, naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo.

52 Cifukwa cace anawafunsa ora lace anayamba kuciralo. Pamenepo anati kwa iye, kuti, Dzulo, ora lacisanu ndi ciwiri malungo anamsiya.

53 Cifukwa cace atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupira iye yekha ndi a pa banja lace onse.

54 Ici ndi cizindikilo caciwiri Yesu anacita, ataeokera ku Yudeya, ndi kulowa m'Galileya.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21