Yohane 2 BL92

Yesu asandutsa madzi vinyo ku Kana

1 Ndipo tsiku lacitatu pariali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amace wa Yesu anali komweko.

2 Ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ace anaitanidwa ku ukwatiwo.

3 Ndipo pakutha vinyo, amace wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo,

4 Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi inu? nthawi yanga siinafike.

5 Amace ananena kwa atumiki, Cimene ciri conse akanena kwa inu, citani.

6 Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.

7 Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde nde.

8 Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwamkulu wa phwando. Ndipo anapita nao.

9 Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwa kumene anacokera (koma atumiki amene adatiinga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati,

10 nanena naye, Munthu ali yense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.

11 Ciyambi ici ca zizindikilo zace Yesu anacita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wace; ndipo akuphunzira ace anakhulupirira iye.

12 Zitapita izianatsikira ku Kapemao, iye ndi amace, ndiabale ace, ndi ophunzira ace; nakhala komweko masiku owerengeka.

Yesu ayeretsa Kacisi poyamba paja

13 Ndipo Paskha wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.

14 Ndipo anapeza m'Kacisiiwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi.

15 Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m'Kacisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome;

16 nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Cotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.

17 Akuphunzira ace anakumbukila kuti kunalembedwa, Cangu ca pa nyumba yanu candidya ine.

18 Cifukwa cace Ayuda anayankha nati kwa iye, Mutionetsera ife cizindikilo canji, pakuti mucita izi?

19 Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani kacisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.

20 Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi cimodzi analimkumanga Kacisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu?

21 Koma iye analikunena za kacisi wathupi lace.

22 Cifukwa cace atauka kwa akufa, akuphunzira ace anakumbukira kuti ananena ici; ndipo anakhulupirira colemba, ndi mau amene Yesu ananena.

23 Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paskha paphwando, ambiri anakhulupirira dzinalace, pakuona zizindikilo zace zimene anaeitazi.

24 Koma Yesu sanakhulupirira iwo kuti akhale nao, cifukwa iye anadziwa anthu onse,

25 ndipo sanasowa wina acite umboni za munthu; pakuti anadziwa iye yekha cimene cinali mwa munthu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21