Yohane 14 BL92

Yesu aneneratu za kubweranso kwace

1 Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.

2 M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.

3 Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.

4 Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace.

5 Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji?

6 Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

Yesu ndi Atate ndiwo amodzi

7 Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye.

8 Filipo ananena ndi iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira.

9 Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?

10 Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace.

11 Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe.

12 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, nchito zimene ndicita Ine adzazicitanso iyeyu; ndipo adzacita zoposa izi; cifukwa ndipita Ine kwa Atate.

13 Ndipo cimene ciri conse mukafunse m'dzina langa, ndidzacicita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.

14 Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzacita.

15 Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.

Lonjezo la Mzimu Woyera

16 Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse,

17 ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.

18 Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu.

19 Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.

20 Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.

21 Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye.

22 Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?

23 Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.

24 Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo 1 mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.

25 Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.

26 Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.

Mphatso ya mtendere

27 4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.

28 Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, 6 Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; 7 pakuti Atate ali wamkuru ndi Ine.

29 Ndipo tsopano 8 ndakuuzani cisanacitike, kuti pamene citacitika mukakhulupire.

30 Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti 9 mkuru wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;

31 koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndikuti 10 ndicita monga momwe Atate wandilamulira. Nyamukani, tizimuka kucokera kuno.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21