Yohane 10 BL92

Za Mbusa Wabwino

1 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.

2 Koma iye wakulowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa.

3 Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ace; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.

4 Pamene adaturutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zimtsata iye; cifukwa zidziwa mau ace.

5 Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; cifukwasizidziwa mau a alendo.

6 Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao.

7 Cifukwa cace Yesuananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.

8 Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo.

9 Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa, nadzaturuka, nadzapeza busa.

10 Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka.

11 Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa.

12 Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa siziri zace za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;

13 cifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.

14 Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira ine,

15 monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga cifukwa ca nkhosa.

16 Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi,

17 Cifukwa ca ici Atate andikonda Ine, cifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso,

18 Palibe wina andicotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndiri nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndiri nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa. Atate wanga.

19 Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda cifukwa ca mau awa.

20 Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi ciwanda, nacita misala; mukumva iye bwanji?

21 Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa ciwanda. Kodi ciwanda cikhoza kumtsegulira maso wosaona?

Yesu adziulula ali Mwana wa Mulungu

22 Koma kunali phwando la kukonzersanso m'Yerusalemu; nyengoyo ndi yacisanu.

23 Ndipo Yesu analikuyendayenda m'Kacisi m'khumbi la Solomo,

24 Pamenepo Ayuda anamzungulira iye, nanena ndi iye, Kufikira liti musfnkhitsa-slnkhitsa moyo wathu? ngati Inu ndinu Kristu, tiuzeni momveka.

25 Yesu anayankha iwo, Ndakuuzani, ndipo simukhulupirira, Nchitozi ndizicita Ine m'dzina la Atate wanga, zimenezi zindicitira umboni.

26 Koma inu simukhulupira, cifukwa simuli a mwa nkhosa zanga.

27 Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.

28 Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka ku nthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa,

29 Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m'dzanja la Atate.

30 Ine ndi Atate ndife amodzi.

31 Ayuda anatolanso miyala kuti amponye iye.

32 Yesu anayankha iwo, ndakuonetsani inu nchito zabwino zambiri za kwa Atate; cifukwa ca nchito yiti ya izo mundiponya miyala?

33 Ayuda anamyankha iye, Cifukwa ca nchito yabwino sitikuponyani miyala, koma cifukwa ca mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu,

34 Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'cilamulo canu, Ndinati Ine, Muli milungu?

35 Ngati anawacha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo colemba sicingathe kutyoka),

36 kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma ku dziko lapansi, Ucita mwano; cifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?

37 Ngati sindicita nchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine.

38 Koma ngati ndicita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani nchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi ine mwa Atate.

39 Anafunanso kumgwira iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao.

40 Ndipo anacoka kunkanso tsidya lija la Yordano, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.

41 Ndipo ambiri anadza kwa iye; nanena kuti, Sanacita cizindikilo Yohane; koma zinthu ziri zonse Yohane ananena za iye zinali zoona.

42 Ndipo ambiri anakhulupirira iye komweko.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21