Yohane 5 BL92

Yesu aciritsa wopuwala ku thamanda La Betesda

1 Zitapita izi panali phwando la Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.

2 Koma pali thamanda m'Yerusalemu pa cipata ca nkhosa, lochedwa m'Cihebri Betesda, liri ndi makumbi asanu.

3 M'menemo munagona khamu lalikuru la anthu odwala akhungu, opunduka miyendo, opuwala. [

4 ]

5 Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwace zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.

6 Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikuru pamenepo, ananena naye, Ufuna kuciritsidwa kodi?

7 Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndiribe wondibvika ine m'thamanda, pali ponse madzi abvundulidwa; koma m'mene ndirinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine.

8 Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende,

9 Ndipo pomwepo munthuyu anacira, nayalula mphasa yace, nayenda.Koma tsiku lomwelo linali la Sabata.

10 Cifukwa cace Ayuda ananena kwa wociritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.

11 Koma iyeyu anayankha iwo, iye amene anandiciritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende,

12 Anamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende?

13 Koma wociritsidwayo sanadziwa ngati ndani; pakuti Yesu anacoka kacetecete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.

14 Zitapita izi Yesu anampeza m'Kacisi, nati kwa iye, Taona, waeiritsidwa; usacimwenso, kuti cingakugwere ecipa coposa.

15 Munthuyo anacoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adameiritsa.

Yesu adziulula kuti ali Mwana wa Mulungu

16 Ndipo cifukwa ca ici Ayuda analondalonda Yesu, popeza anacita izo dzuwa la Sabata.

17 Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira nchito kufikira tsopano, lnenso ndigwira nchito.

18 Cifukwa ca ici Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si cifukwa ca kuswa dzuwa la Sabata kokha, komatu amaehanso Mulungu Atate wace wa iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.

19 Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kucita kanthu pa yekha, koma cimene aona Atate acicita, ndico. Pakuti zimene iye azicita, zomwezo Mwananso azicita momwemo.

20 Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azicita yekha: ndipo adzamuonetsa nchito zoposa izi, kuti mukazizwe,

21 Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwanaapatsa moyo iwo amene iye afuna.

22 Pakuti Atate saweruza munthu ali yense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana;

23 kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma iye.

24 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wacokera kuimfa, nalowa m'moyo.

25 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.

26 Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha;

27 ndipo anampatsa iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.

28 Musazizwe ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ace,

29 nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.

30 Sindikhoza kucita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; cifukwa kuti sinditsata cifuniro canga, koma cifuniro ca Iye ondituma Ine.

31 Ngati ndicita umboni wa Ine ndekha, umboni wanga suli woona.

32 Wocita umboni wa Ine ndi wina; ndipo ndidziwa kuti umboni umene iye andicitira Ine uli woona.

33 Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anacitira umboni coonadi.

34 Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu: koma ndinena izi, kuti inu mukapulumutsidwe.

35 Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwace kanthawi.

36 Koma Ine ndiri nao umboni woposa wa Yohane; pakuti nchito zimene Atateanandipatsa ndizitsirize, nchito zomwezo ndizicita zindicitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.

37 Ndipo Atate wonditumayo, 1 Iyeyu wandicitira Ine umboni. Simunamva mau ace konse, kapena maonekedwe ace simunaona.

38 Ndipo mulibe mau ace okhala mwa inu; cifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.

39 2 Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundicitira Ine umboni ndi iwo omwewo;

40 ndipo 3 simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo.

41 4 Ulemu sindiulandira kwa anthu.

42 Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe cikondiea Mulungu mwa inu nokha.

43 Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lace la iye mwini, iyeyu mudzamlandira.

44 Mungathe inu bwanji kukhulupira, 5 popeza mulandira ulemu wina kwa mnzace ndipo ulemu wakucokera kwa Mulungu yekha simuufuna?

45 Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; 6 pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama.

46 Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; 7 pakuti iyeyu analembera za Ine.

47 Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mau anga?

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21