Yohane 15 BL92

Mpesa ndi nthambi zace

1 Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.

2 Nthambi iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka.

3 Mwakhala okonzeka tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu,

4 Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.

5 Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kucita kanthu.

6 Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.

7 Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu.

8 Mwa ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.

9 Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'cikondi canga.

10 Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'cikondi canga; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'cikondi cace.

11 Izi ndalankhula ndi inu, kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, ndi kuti cimwemwe canu cidzale.

12 Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzace, monga ndakonda inu.

13 Palibe munthu ali naco cikondi coposa ici, cakuti munthu ataya moyo wace cifukwa ca abwenzi ace.

14 Muli abwenzianga inu, ngati muzicita zimene ndikulamulirani inu.

Ciyanjano catsopano

15 Sindichanso inu akapolo; cifukwa kapolo sadziwa cimene mbuye wace acita; koma ndacha inu abwenzi; cifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.

16 Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala cipatso, ndi kuti cipatso canu cikhale; kuti cimene ciri conse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.

17 Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzace.

Wokhulupirira pokhala pa dziko lapansi

18 Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.

19 Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zace za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, cifukwa ca ici likudani inu.

20 Kumbukilani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.

21 Koma izi zonse adzakucitirani cifukwa ca dzina langa, cifukwa sadziwa wondituma Ine.

22 Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo cimo; koma tsopano alibe cowiringula pa macimo ao.

23 Iye wondida Ine, adanso Atate wanga.

24 Sindikadacita mwa iwo nchito zosacita wina, sakadakhala nalo cimo; koma tsopano anaona, nada: Ine ndi Atate wanganso,

25 Koma citero, kuti mau olembedwa m'cilamulo cao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda cifukwa.

Mzimu Woyera ndi akuphunzira omwe adzacita umboni

26 Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kucokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa coonadi, amene aturuka kwa Atate, Iyeyu adzandicitira Ine umboni.

27 Ndipo inunso mucita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira ciyambi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21