Yohane 7 BL92

Abale a Yesu sambvomereza

1 Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m'Galileya; pakuti sanafuna kuyendayenda m'Yudeya, cifukwa Ayuda anafuna kumupha iye.

2 Koma phwando la Ayuda, phwando la misasa, linayandikira.

3 Cifukwa cace abale ace anati kwa iye, Cokani pano, mumuke ku Yudeya, kuti akuphunzita anunso akapenye nchito zanu zimenemucita.

4 Pakuti palibe munthu acita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera, Ngati mucita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi,

5 Pakuti angakhale abale ace sanakhulupirira iye.

6 Cifukwa cace Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse.

7 Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilicitira umboni, kuti nchito zace ziri zoipa,

8 K werani inu kunka kuphwando; sindikwera Ineku phwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.

9 Ndipo m'mene adanena nao zimenezi anakhalabe m'Galileya,

Yesu aphunzitsa m'Kacisi. Ayesa kumgwira

10 Koma pamene abale ace adakwera kunka kuphwando, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika.

11 Pomwepo Ayuda analikumfuna iye paphwando, nanena, Ali kuti uja?

12 Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, lai, koma asoceretsa khamu la anthuwo.

13 Cinkana anatero panalibe munthu analankhula za iye poyera, cifukwa ca kuopa Ayuda.

14 Koma pamene padafika pakati pa phwando, Yesu anakwera nalowa m'Kacisi, naphunzitsa,

15 Cifukwa cace Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?

16 Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, koma ca iye amene anandituma Ine.

17 Ngati munthu ali yense afuna kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco, ngati cicokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zocokera kwa Ine ndekha.

18 Iye wolankhula zocokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha, iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa iye mulibecosalungama.

19 Si Mose kodi anakupatsani inu cilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu acita cilamulo? Mufuna kundipha cifukwa ninji?

20 Khamu la anthu linayankha, Muli ndi ciwanda: afuna ndani kukuphani lou?

21 Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinacita nchito imodzi, ndipo muzizwa monse,

22 Cifukwa ca ici Mose, anakupatsani inu mdulidwe (si kuti ucokera kwa Mose, koma kwa, makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.

23 Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti cilamulo ca Mose cingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, cifukwa ndamciritsadi munthu tsiku la Sabata?

24 Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani ciweruziro colungama.

25 Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha r

26 ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akuru adziwa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?

27 Koma ameneyo tidziwa uko acokera: koma Kristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko acokera.

28 Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.

29 Ine ndimdziwa iye; cifukwa ndiri wocokera kwa iye, nandituma Ine Iyeyu.

30 Pamenepo anafuna kumgwira iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, cifukwa nthawi yace siinafike.

31 Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira iye; ndipo ananena, Pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita ameneyo?

32 Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire iye.

33 Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma Ine.

34 Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo.

35 Cifukwa cace Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza iye? kodi adzamuka kwa Ahelene obalalikawo, ndi kuphunzitsa Ahelene?

36 Mau awa amene ananena ndi ciani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo?

Yesu aneneratu za Mzimu Woyera

37 Koma tsiku lomariza, lalikurulo la phwando, Yesu anaimirira napfuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva Ludzu, adze kwa Ine, namwe.

38 Iye wokhulupirira Ine, monga cilembo cinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kuturuka m'kati mwace.

39 Koma 1 ici anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, cifukwa Yesu sanalemekezedwa panthawi pomwepo.

Anthu atsutsana za Iye

40 Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, 2 Mnene riyo ndi uyu ndithu.

41 Ena ananena, 3 Uyu ndi Kristu, Koma ena ananena, Kodi Kristu adza kuturuka m'Galileya?

42 4 Kodi sicinati cilembo kuti Kristu adza kuturuka mwa mbeu ya Davine, ndi kucokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davine?

43 5 Kudakhala tsono kusiyana m'khamulo cifukwa ca iye.

44 Koma 6 ena mwa iwo anafuna kumgwira iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.

45 Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga iye bwanji?

46 Anyamatawo anayankha, 7 Nthawi yonse palibe munthu analankhula cotero.

47 Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso?

48 8 Kodi wina wa akuru anakhulupirira iye, kapena wa Afarisi?

49 Koma khamu ili losadziwa cilamulo, likhala lotembereredwa.

50 9 Nikodemo ananena kwa iwo, amene uja adadza kwa iye kale, ali mmodzi wa iwo,

51 Kodi cilamulo cathu ciweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira cimene, acita?

52 Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli woturuka m'Galileya? Santhula, nuone kuti m'Galileya sanauka mneneri.

53 Ndipo anamuka munthu yense ku nyumba yace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21