Yohane 8 BL92

Za mkazi wacigololo

1 Koma Yesu anamuka ku phiri la Azitona.

2 Komac mamawa anadzanso kuKacisi, ndipo anthu onse anadza kwa iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.

3 Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa iye mkazi wogwidwa m'cigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati,

4 ananena kwa iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkucita cigololo.

5 Koma m'cilamulo Mose anatilamulira, ttwaponye miyala otere. Cifukwa cace Inu munena ciani za iye?

6 Koma ici ananena kuti amuyese iye, kuti akhale naco comneneza iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi cala cace.

7 Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda cimo, ayambe kumponya mwala,

8 Ndipo m'mene adaweramanso analemba ndi cala cace pansi.

9 Koma iwo, m'mene adamva, anaturukamo amodzi amodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.

10 Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?

11 Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usacimwenso.

Yesu wotumidwa ndi Atate

12 Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.

13 Cifukwa cace Afarisi anati kwa iye, Mucita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli woona.

14 Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndicita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; cifukwa ndidziwa kumene ndinacokera ndi kumene ndimukako; koma e inu, simudziwa kumene ndicokera, ndi kumene ndimukako.

15 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.

16 Ndipo ngati ndiweruza Ine, ciweruziro canga ciri coona; pakuti sindiri pa ndekha, koma ine ndi Atate amene anandituma Ine.

17 Inde kudalembedwa m'cilamulo canu kuti umboni wa anthu awiri uli woona.

18 Ine ndine wakucita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine, acita umboni wa Ine.

19 Cifukwa cace ananena ndi iye, Ali kuti Atate, wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukada-dziwanso Atate wanga.

20 Mau awa analankhula m'nyumba ya cuma ca Mulungu pophunzitsa m'Kacisi; ndipo palibe munthu anamgwira iye, pakuti nthawi yace siinafike.

21 Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'cimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.

22 Cifukwa cace Ayuda ananena, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?

23 Ndipo ananena nao, Inu ndinu ocokera pansi; Ine ndine wocokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindiri Ine wa dziko lino lapansi.

24 Cifukwa cace ndinati kwa inu, kuti mudzafam'macimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'macimo anu.

25 Pamenepo ananena kwa iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Cimene comwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira paciyambi.

26 Ndiri nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa iye, zomwezo ndilankhuia kwa dziko lapansi.

27 Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate.

28 Cifukwa cace Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindicita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.

29 Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiya Ine pa ndekha; cifukwa ndicita Ine rimene zimkondweretsa iye nthawi zonse.

30 Pakulankhula iye zimenezi, ambiri anakhulupirira iye.

31 Cifukwa cace Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli akuphunzira anga ndithu;

32 ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

33 Anamyankha iye, Tiri mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yonse; munena bwanji; Mudzayesedwa aufulu?

34 Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakucita cimo ali kapolo wa cimolo.

35 Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse.

36 Cifukwa cace ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

37 Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamuj koma mufuna kundipha Ine, cifukwa mau anga alibe malo mwa inu.

38 1 Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso mucita cimene mudamva kwa atate wanu.

39 Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, 2 Ngati muli ana a Abrahamu, mukadacita nchito za Abrahamu.

40 Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu coonadi, 3 cimene ndinamva kwa Mulungu; ici Abrahamu sanacita.

41 Inu mucita nchito za atate wanu. Anati kwa iye, Sitinabadwa ife m'cigololo; tiri naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.

42 Yesu anati kwa iwo, 4 Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinaturuka, ndi kucokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.

43 Simuzindikira malankhulidwe anga cifukwa ninji? Cifukwa simungathe kumva mau anga,

44 5 Inu muli ocokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zace za atate wanu mufuna kucita. Iyeyu anali wambanda kuyambira paciyambi, ndipo sanaima m'coonadi, pakuti mwa iye mulibe coonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wace; pakuti ali wabodza, ndi atate wace wa bodza.

45 Koma Ine, cifukwa ndinena coonadi, simukhulupirira Ine.

46 Ndani mwa inu anditsutsa Ine za cimo? Ngati ndinena coonadi, simundikhulupirira Ine cifukwa ninji?

47 6 Iye wocokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva cifukwa cakuti simuli a kwa Mulungu,

48 Ayuda anayankha nati kwa iye, Kodi sitinenetsa kun Inu ndinu Msamariya, ndipo 7 muli ndi ciwanda?

49 Yesu anayankha, Ndiribe ciwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.

50 Koma 8 Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza.

51 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 9 Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.

52 Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi ciwanda. 10 Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.

53 Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?

54 Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli cabe; 11 Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za iye, kuti ndiye Mulungu wanu;

55 ndipo 12 inu simunamdziwa iye; koma Ine ndimdziwa iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa iye, ndidzakhala wonama cimodzimodzi inu; koma ndimdziwa iye, ndipo ndisunga mau ace.

56 13 Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona, nasangalala.

57 Ayuda pamenepo anati kwa iye, Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi?

58 Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo 14 Ine ndiripo.

59 Pamenepo 15 anatola miyala kuti amponye iye; koma Yesu anabisala, naturuka m'Kacisi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21