1 Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona cibadwire.
2 Ndipo akuphunzira ace anamfunsa iye, nanena, Rabi, anacimwa ndani, ameneyo, kapena atate wace ndi amace, kuti anabadwa wosaona?
3 Yesu anayankha, Sanacimwa ameneyo, kapena atate wace ndi amace; koma kuti nchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.
4 Tiyenera kugwira nchito za iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira nchito,
5 Pakukhala Ine m'dziko lapansi, ndiri kuunika kwa dziko lapansi.
6 Pamene ananena izi, analabvula pansi, nakanda thope ndi malobvuwo, napaka thopelo m'maso,
7 nati kwa iye, Muka, kasambe m'thamanda la Siloamu (ndilolosandulika, Wotumidwa). Pamenepo anacoka, nasamba, nabwera alikuona.
8 Cifukwa cace anzace ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?
9 Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, lai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene.
10 Pamenepo ananena ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji?
11 Iyeyu anayankha, Munthuyo wochedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; cifukwa cace ndinacoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya,
12 Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine.
13 Anapita naye amene anali wosaona kale kwa Afarisi.
14 Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ace.
15 Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera, Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.
16 Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sacokera kwa Mulungu, cifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wocimwa, akhoza bwanji kucita zizindikilo zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.
17 Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri.
18 Cifukwa cace Ayuda sanakhulupirira za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wace ndi amace a iye wopenya;
19 nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona?
20 Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wace ndi amace anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona;
21 koma sitidziwa umo apenyera tsopano; kapena sitimdziwa amene anamtsegulira pamaso pace; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.
22 Izi ananena atate wace ndi amace, cifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu ali yense adzambvomereza iye kuti ndiye Kristu, akhale woletsedwa m'sunagoge,
23 Cifukwa ca ici atate wace ndi amace anati, Ali wamsinkhu; mumfunse iye.
24 Pamenepo anamuitana kaciwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wocimwa.
25 Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wocimwa, sindidziwa; cinthu cimodzi ndicidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya.
26 Cifukwa cace anati kwa iye, Anakucitira iweciani? anakutsegulira iwe maso bwanji?
27 Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamva; mufuna kumvanso bwanji? kodi inunso mufuna kukhala: akuphunzira ace?
28 Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife akuphunzira a Mose.
29 Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene acokera ameneyo,
30 Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti cozizwa ciri m'menemo, kuti inu simudziwa kumene acokera, ndipo ananditsegulira maso anga.
31 Tidziwa kuti Mulungu samvera ocimwa. Koma ngati munthu ali yense akhala wopembedza Mulungu nacita cifuniro cace, amvera ameneyo.
32 Kuyambira paciyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona cibadwire.
33 Ngatiuyu sanacokera kwa Mulungu, sakadakhoza kucita kanthu.
34 Anayankha natikwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.
35 Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupirira Mwana wa Mulungu?
36 Iyeyu anayankha nati, Ndipo ndani iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire iye?
37 Yesu anati kwa iye, Wamuona iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo.
38 Koma iye anati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo anamgwadira iye.
39 Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine ku dziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona,
40 Ndipo Afarisi ena akukhala ndi iye anamva izi, nati kwa iye, Kodi ifenso ndife osaona?
41 Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo cimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: cimo lanu likhala.