Yohane 19 BL92

1 Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.

2 Ndipo asilikari, m'mene analuka korona waminga anambveka pamutu pace, nampfunda iye maraya acibakuwa;

3 nadza kwa iye, nanena, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda! nampanda khofu.

4 Ndipo Pilato anaturukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa iye cifukwa ciri conse.

5 Pamenepo Yesu anaturuka kunja, atabvala korona waminga; ndi maraya acibakuwa, Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!

6 Ndipo pamene ansembe akulu ndi anyamata anamuona iye, anapfuula nanena, Mpacikeni, mpacikeni, Pilato ananena nao, Mtengeni iye inu nimumpaeike; pakuti ine sindipeza cifukwa mwa: iye.

7 Ayuda anamyankha iye, Tiri naco cilamulo ife, ndipo monga mwa cilamuloco ayenera kufa, cifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.

8 Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa.

9 Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Mucoka kuti? koma Yesu sanamyankha kanthu.

10 Cifukwa cace Pilato ananena kwa iye, Simulankhula ndi ine kodi? simudziwa kodi kuti ulamuliro ndiri nao wakukumasulani, ndipo ndiri nao ulamuliro wakukupacikani?

11 Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kucokera Kumwamba; cifukwa ca ici iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo cimo loposa.

12 Pa ici Pilato anafuna kumasula iye; koma Ayuda anapfuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.

13 Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anaturuka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lace; Bwalo lamiyala, koma m'Cihebri, Gabata,

14 Koma linali tsiku lokonza Paskha; panali monga ora lacisanu ndi cimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, Mfumu yanu!

15 Pamenepo anapfuula iwowa, Cotsani, Cotsani, mpacikeni iye! Pilato ananena nao, Ndipacike Mfumu yanu kodi? Ansembe akulu anayankha, Tiribe Mfumu koma Kaisara.

16 Ndipo pamenepo anampereka iye kwa iwo kutiampacike,Pamenepo anatenga Yesu;

Ampacika Yesu pamtanda

17 ndipo anasenza mtanda yekha, naturuka kunka ku malo ochedwa Maloa-bade, amene achedwa m'Cihebri, Golgota:

18 kumene anampacika Iye; ndipo pamodzi ndi iye awiri ena, cakuno ndi cauko, koma Yesu pakati.

19 Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA.

20 Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; cifukwa malo amene Yesu anapaeikidwapo anali pafupipa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Cihebri, ndi m'Ciroma, ndi m'Cihelene.

21 Pamenepo ansembe akulu a Ayuda, ananena kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndiri Mfumu ya Ayuda.

22 Pilato anayankha, Cimene ndalemba, ndalemba.

23 Pamenepo asilikari, m'mene adapacika Yesu, anatenga zobvala zace, nadula panai, natenga wina cina, wina cina, ndiponso maraya; koma maraya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pace, analibe msoko.

24 Cifukwa cace anati wina kwa mnzace, Tisang'ambe awa, koma ticite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zobvala zanga mwa iwo okha, ndi pa maraya anga anacitira maere. Ndipo asilikari anacita izi.

25 Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amace, ndi mbale wa amace, Mariya, mkazi wa Kleopa, ndi Mariya wa Magadala.

26 Pamenepo Yesu pakuona amace, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amace, Mkazi, taonani, mwana wanu!

27 Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.

28 Citapita ici Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepokuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.

29 Kunaikidwako cotengera codzala ndi vinyo wosasa; cifukwa cace anazenenga cinkhupule codzaza ndi vinyo wosasayo pa phesi lahisope, nacifikitsa kukamwa kwace.

30 Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.

Satyola miyendo ya Yesu

31 Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti 1 mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikuru, anapempha Pilato kuti miyendo yao ityoledwe, ndipo acotsedwe.

32 Cifukwa cace anadza asilikari natyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopacikidwa pamodzi ndi iye;

33 koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona iye, kuti wafa kale, sanatyola miyendo yace;

34 koma mmodzi wa asilikari anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yace, ndipo 2 panaturuka pomwepo mwazi ndi madzi.

35 Ndipo 3 iye amene anaona, wacita umboni, ndi umboni wace uti woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupire.

36 Pakuti izi zinacitika, kuti lembo likwaniridwe, 4 Pfupa la iye silidzatyoledwa.

37 Ndipo linenanso lembo lina, 5 Adzayang'ana pa iye amene anampyoza.

Kuikidwa kwa Yesu

38 6 Citatha ici. Y osefe wa ku Arimateya, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, cifukwa ca kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akacotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Cifukwa cace anadza, nacotsa mtembo wace.

39 Koma anadzanso 7 Nikodemo, amene anadza kwa iye usiku poyamba paja, alikutenga cisanganizo ca mure ndi aloe, monga miyeso zana.

40 Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsaru zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.

41 Koma kunali munda kumalo kumene anapacikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwamo munthu ali yense nthawi zonse.

42 8 Pomwepo ndipo anaika Yesu, cifukwa ca tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21