Yohane 16 BL92

Awacenjeza za kuzunzidwa

1 Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe.

2 Adzakuturutsani m'masunagoge; koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu,

3 Ndipo izi adzacita, cifukwa sanadziwa Atate, kapena Ine.

4 Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira paciyambi, cifukwa ndinali pamodzi ndi inu.

5 Koma tsopano ndimuka kwa iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Munka kuti?

6 Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala mumtima mwanu.

Comwe Mzimu Woyera adzacitira anthu

7 Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.

8 Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro;

9 za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine;

10 za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso;

11 za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa.

12 Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.

13 Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani.

14 Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

15 Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; cifukwa cace ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

Yesu anena za imfa, kuuka, ndikubwera kwace

16 Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiona Ine.

17 Mwa akuphunzira ace tsono anati wina ndi mnzace, ici nciani cimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, cifukwa ndimuka kwa Atate?

18 Cifukwa cace ananena, ici nciani cimene anena, Kanthawi? Sitidziwa cimene alankhula.

19 Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzace za ici, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?

20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzacita cisoni inu, koma cisoni canu cidzasandulika cimwemwe.

21 Mkazi pamene akuti abale ali naco cisoni, cifukwa yafika nthawi yace; koma pamene wabala mwana, sakumbukilanso kusaukako, cifukwa ca cimwemwe kuti wabadwa munthu ku dziko lapansi.

22 Ndipo inu tsono muli naco cisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzacotsa kwa inu cimwemwe canu.

23 Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.

24 Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti cimwemwe canu cikwaniridwe.

25 Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.

26 Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate;

27 pakuti Atate yekha akonda inu, cifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinaturuka kwa Atate.

28 Ndinaturuka mwa Atate, ndipo ndadza ku dziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.

29 Akuphunzira ace ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena ciphiphiritso,

30 Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ici tikhulupirira kuti munaturuka kwa Mulungu.

31 Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano?

32 Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zace za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, cifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,

33 Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21