Yohane 13 BL92

Yesu asambitsa mapazi a anyamata ace

1 Koma pasanafike phwando la Paskha, Yesu, podziwa kuti nthawi yace idadza yakucoka kuturuka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ace a iye yekha a m'dziko lapansi, anawakomia kufikira cimariziro.

2 Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adathakuika mu mtima wace wa Yudase mwana wa Simoni Isikariote, kuti akampereke iye,

3 Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa iye zonse m'manja mwace, ndi kuti anacokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,

4 ananyamuka pamgonero, nabvula malaya ace; ndipo m'mene adatenga copukutira, anadzimanga m'cuuno.

5 Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ace, ndi kuwapukuta ndi copukutira, cimene anadzimanga naco,

6 Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?

7 Yesu anayankha nati kwa iye, Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwace.

8 Petro ananena ndi iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine.

9 Simoni Petro ananena ndi iye, Ambuye, si mapazi anga okha, komanse manja ndi mutu.

10 Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.

11 Pakuti anadziwa amene adzampereka iye; cifukwa ca ici anati, Simuli oyera nonse.

12 Pamenepo, atatha iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ace, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga cimene ndakucitirani inu; mucizindikira kodi?

13 Inu mundicha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.

14 Cifukwa cace, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzaceo

15 Pakuti ndakupatsani inu citsanzo, kuti, monga Ine ndakucitirani inu, inunso mucite.

16 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wace; kapena mtumwi sali wamkuru ndi womtuma iye,

17 Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzicita.

18 Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti colemba cikwaniridwe, iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine cinendene cace.

19 Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, cisadacitike, kuti pamene citacitika, mukakhulupire kuti ndine amene.

20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene ali yense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.

Yesu aneneratu kuti Yudase adzampereka

21 Yesu m'mene adanenaizi, anabvutika mumzimu, nacita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.

22 Akuphunzira analikupenyanawina kwa mnzace, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani.

23 Koma mmodzi wa akuphunzira ace, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa cifuwa ca Yesu.

24 Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.

25 Iyeyu potsamira pomwepo, pa cifuwa ca Yesu, anena ndi iye. Ambuye, ndiye yani?

26 Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa, Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudase mwana wa Simoni Isikariote.

27 Ndipopambuyo pace pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Cimene ucita, cita msanga,

28 Kama palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa cimene anafuna, poti atere naye.

29 Pakuti popeza Yudase anali nalo thumba, enaanalikuyesakuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa paphwando; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.

30 Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anaturuka pomwepo, Koma kunali usiku.

31 Tsono m'mene adaturuka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa iye;

32 ndipo Mulungu adzamlemekeza iye mwa iye yekha, adzamlemekeza iye tsopano apa.

33 Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.

34 Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace.

35 1 Mwa ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace.

Yesu aneneratu kuti Petro adzamkana

36 Simoni Petro anena ndi iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, 2 udzanditsata bwino lomwe.

37 Petro ananena ndi iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano cifukwa ninji? 3 Ndidzataya moyo wanga cifukwa ca Inu.

38 Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya cifukwa ca Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21