Yohane 11 BL92

Ciukitso ca Lazaro

1 Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Mariya ndi mbale wace Marita.

2 Koma ndiye Mariya uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ace ndi tsitsi lace, amene mlongo wace Lazaro anadwala.

3 Pamenepo alongo ace anatumiza kwa iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.

4 Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma cifukwa ca ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.

5 Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wace, ndi Lazaro.

6 Cifukwa cace pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri.

7 Ndipo pambuyo pace ananena kwa akuphunzira ace, Tiyeni tipitenso ku Yudeya.

8 Akuphunzira ananena ndi iye, Ambuye, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?

9 Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, cifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi,

10 Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, cifukwa mulibe kuunika mwa iye.

11 Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo tace.

12 Cifukwa cace akuphunzira ace anati kwa iye, Ambuye, ngati ali m'tulo adzacira.

13 Koma Yesu adanena za imfa yace; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.

14 Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.

15 Ndipo ndikondwera cifukwa ca inu kuti kunalibe Ine komweko, cakuti mukakhulupire; koma tiyeni, tipite kwa iye.

16 Pamenepo Tomasi, wochedwa Didimo, anati kwa akuphunzira anzace, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.

17 Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai.

18 Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yace yonga ya mastadiya khumi ndi asanu;

19 koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.

20 Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi iye; koma Mariya anakhalabe m'nyumba.

21 Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.

22 Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu.

23 Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka.

24 Marita ananena ndi iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomariza.

25 Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;

26 ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ici?

27 Ananena ndi iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.

28 Ndipo m'mene anati ici anacoka naitana Mariya mbale wace m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.

29 Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa iye.

30 (Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye)

31 Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.

32 Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.

33 Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika mwini,

34 nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni, mukaone.

35 Yesu analira.

36 Cifukwa cace Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi!

37 Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sanakhoza kodi kucita kuti sakadafa ameneyunso?

38 Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo.

39 Yesu ananena, Cotsani mwala. Marita, mlongo wace wa womwalirayo, ananena ndi iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.

40 Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero wa Mulungu?

41 Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.

42 Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma cifukwa ca khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ici, kuti akhulupire kuti Inu munandituma Ine.

43 Ndipom'mene adanena izi, ana pfuula ndi mau akuru, Lazaro, turuka.

44 Ndipo womwalirayo anaturuka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yace inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.

45 Cifukwa cace ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Mariya, m'mene anaona cimene anacita, anakhulupirira iye.

46 Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazicita.

Afarisi apangana za kupha Yesu

47 Pamenepo ansembe akulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? cifukwa munthu uyu acita zizindikilo zambiri.

48 Ngati timleka iye kotero, onse adzakhulupirira iye; ndipo adzadza Aroma nadzacotsa malo athu ndi mtundu wathu.

49 Koma wina mmodzi wa mwa iwo, Kayafa, wokhaia mkulu wa ansembe caka comweco anati kwa iwo, Simudziwa kanthu konse inu,

50 kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke,

51 Koma ici sananena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe caka comweco ananenera kuti Yesu akadzafera mtunduwo;

52 ndipo si cifukwa ca mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo.

53 Cifukwa cace, kuyambira tsiku Iomwelo anapangana kuti amuphe iye.

54 Cifukwa cace Yesu sanayandeyendanso poonekera mwa Ayuda, koma anacokapo kunka ku dziko loyandikira cipululu, kumudzi dzina lace Efraimu; nakhala komweko pamodzi ndi akuphunzira ace.

55 Koma Paskha wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kucoka ku miraga, usanafike Paskha, kukadziyeretsa iwo okha.

56 Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzace poimirira iwo m'Kacisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuphwando kodi?

57 Koma ansembe akulu ndi Afarisi adalamulira, kuti, munthu wina akadziwa pokhala iye, aulule, kuti akamgwire iye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21