Yohane 17 BL92

Yesu apempherera akuphunzira ace

1 Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ace Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeoi Inu;

2 monga mwampatsa iye ulamuliro pa thupi liri lonse, kuti onse amene mwampatsa iye, awapatse iwo moyo wosatha.

3 Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.

4 Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m'mene ndinatsiriza nchito imene munandipatsa ndicite.

5 Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.

6 Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu.

7 Azindikira tsopane kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine zicokera kwa Inu;

8 cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti Inu munandituma Ine.

9 Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine,

10 cifukwa ali anu: ndipo zanga zonse ziri zanu, ndi zanu ziri zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo.

11 Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate. Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.

12 Pamenendinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa citayiko, kuti lembo likwaniridwe.

13 Koma tso pane ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale naco cimwemwe canga cokwaniridwa mwa iwo okha.

14 Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi linadana nao, cifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.

15 Sindipempha kuti muwacotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.

16 Siali adziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.

17 Patulani iwo m'coonadi; mau anu ndi coonadi.

18 Monga momwe munandituma Ine ku dziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo ku dziko lapansi,

19 Ndipo cifukwa ca iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'coonadi.

20 Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine cifukwa ca mau ao;

21 kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupire kuti Inu munandituma Ine.

22 Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa Iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tiri mmodzi;

23 Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kutr dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine,

24 1 Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndiri Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; 2 pakuti munandikonda Inelisanakhazildke dziko lapansi.

25 Atate wolungama, 3 dziko lapansi silinadziwa Inu, koma 4 Ine ndinadziwa Inu; ndipo 5 iwo anazindikira kuti munandituma Ine;

26 ndipo 6 ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti cikondi 7 cimene munandikonda naco cikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21