1 Koma Saulo, wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsya ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,
2 napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.
3 Ndipo poyenda ulendo wace, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kocokera kumwamba;
4 ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?
5 Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;
6 komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.
7 Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.
8 Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.
9 Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.
10 Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,
11 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera
12 ndipo anaona mwamuna dzina, lace Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.
13 Ndipo Hananiya anayankha nati, Ambuye ndamva ndi ambiri za munthu uyu kuti anacitiradi coipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;
14 ndi kuti pane ali nao ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.
15 Koma Ambuye anat kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye cotengera canga cosankhika, cakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli;
16 pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambirl ayenera iye kuzimva kuwawa cifukwaca dzina langa.
17 Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.
18 Ndipo pomwepo padagwa kucoka m'maso mwace ngati mamba, ndipo anapenyanso;
19 ndipo ananyamuka nabatizidwa; ndipo analandira cakudya, naona naco mphamvu.Ndipo anakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena.
20 Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu.
21 Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga m'Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe akuru.
22 Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Kristu.
23 Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye;
24 koma ciwembu cao cinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;
25 koma ophunzira ace anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa ndi mtanga,
26 Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.
27 Koma Bamaba anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.
28 Ndipo anali pamodzi nao, nalowa naturuka ku Yerusalemu,
29 nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Aheleniste; koma anayesayesa kumupha iye.
30 Koma m'mene abale anacidziwa, anapita naye ku Kaisareya, namtumiza acokeko kunka ku Tariso.
31 Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.
32 Koma kunali, pakupita Petro ponse ponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhalaku Luda.
33 Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lace Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.
34 Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Kristu akuciritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.
35 Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Luda ndi ku Sarona, natembenukira kwa Ambuye amenewa.
36 Koma m'Yopa munali wophunzira dzina lace Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi nchito zabwino ndi zacifundo zimene anazicita.
37 Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'cipinda ca pamwamba.
38 Ndipo popeza Luda ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musacedwa mudze kwa ife.
39 Ndipo Petro anayamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye ku cipinda ca pamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa maraya ndizobvala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.
40 Koma Petro anawaturutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ace; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.
41 Ndipo Petro anamgwiradzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.
42 Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.
43 Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.