Macitidwe 5 BL92

Za Hananiya ndi Safira

1 Koma munthu wina dzina lace Hananiya pamodzi ndi Safira mkazi wace,

2 anagulitsa cao, napatula pa mtengo wace, mkazi yemwe anadziwa, natenga cotsala, naciika pa mapazi a atumwi.

3 Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?

4 Pamene unali nao, sunali wako kodi? ndipo pamene unaugulitsa sunali m'manja mwako kodi? bwanji cinalowa ici mumtima mwako? sunanyenga anthu, komatu Mulungu.

5 Koma Hananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha akuru anagwera onse akumvawo.

6 Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, naturuka naye, namuika.

7 Koma atapita monga maora atatu, ndipo mkazi wace, wosadziwa cidacitikaco, analowa.

8 Ndipo Petro ananena naye, Undiuze, ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo ananena, Inde, wakuti.

9 Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kuturuka nawe.

10 Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ace, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kuturuka naye, namuika kwa mwamuna wace.

11 Ndipo anadza mantha akuru pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumvaizi.

12 Ndipo mwa manja aatumwi zizindikilo ndi zozizwa zambiri zinacitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khumbi la Solomo.

13 Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;

14 ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi;

15 kotero kuti ananyamulanso naturuka nao odwala Ifumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale cithunzi cace cigwere wina wa iwo.

16 Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ocokera ku midzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi obvutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anaciritsidwa onsewa.

Atumwi apulumutsidwa m'ndende, natengedwanso kupita nao ku bwalo la akuru

17 Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a cipatuko ca Asaduki, nadukidwa,

18 nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba.

19 Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawaturutsa, nati,

20 Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m'Kacisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.

21 Ndipo atamva ici, analowa m'Kacisi mbanda kuca, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene analinaye, nasonkhanitsa a bwalo la akuru, ndi akulu onse a ana a Israyeli, natuma kundende atengedwe ajawo.

22 Koma anyamata amene adafikako sanawapeza m'ndende, ndipo pobwera anafotokoza,

23 nanena, Nyumba yandende tinapeza citsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.

24 Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kacisi ndi ansembe akulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ici cidzatani.

25 Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali m'Kacisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.

26 Pamenepo anacoka mdindo pamodzi ndi anyamata; nadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.

27 Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pa bwalo la akuru. Ndipo anawafunsa mkuru wa ansembe,

28 nanena, Tidakulamulirani cilamulire, musaphunzitsa kuchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi ciphunzitso canu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.

29 Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.

30 Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpacika pamtengo.

31 Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lace lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israyeli kulapa, ndi cikhululukiro ca macimo.

32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera iye.

33 Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.

34 Koma ananyamukapo wina pa bwalo la akuru, ndiye Mfarisi, dzina lace Gamaliyeli, mphunzitsi wa cilamulo, wocitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.

35 Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israyeli, kadzicenjerani nokha za anthu awa, cimene muti muwacitire.

36 Pakuti asanafike masiku ana anauka Teuda, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, ciwerengero cao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pacabe.

37 Atapita ameneyo, anauka Yuda wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.

38 Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena nchito iyi icokera kwa anthu, idzapasuka;

39 koma ngati icokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.

40 Ndipo anabvomerezana ndi iye; ndipo m'meheadaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kuchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.

41 Pamenepo ndipo anapita kucokera ku bwalo la akuru, 1 nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa cifukwa ca dzinalo.

42 Ndipo masiku onse, m'Kacisi ndi m'nyumba, 2 sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28