Macitidwe 4 BL92

Petro ndi Yohane ku bwalo la akuru

1 Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa kuKacisi ndi Asaduki anadzako,

2 obvutika mtima cifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.

3 Ndipo anawathira manja, nawaika m'ndende kufikira m'mawa; pakuti mpa madzulo pamenepo.

4 Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupira; ndipo ciwerengero ca amuna cinali ngati zikwi zisanu.

5 Koma panali m'mawa mwace, anasonkhana pamodzi m'Yerusalemu oweruza, ndi akulu, ndi alembi;

6 ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Alesandro, ndi onse amene anali a pfuko la mkulu waansembe.

7 Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwacita ici inu?

8 Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,

9 ngati ife lero tiweruzidwa cifukwa ca nchito yabwino ya pa munthu wodwala, ndi maciritsidwe ace,

10 zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israyeli, kuti m'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, amene inu munampacika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.

11 Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pace ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangondya.

12 Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwanalo.

13 Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.

14 Ndipotu pakuona munthu wociritsidwayoalikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa.

15 Koma pamene anawalamulira iwo acoke m'bwalo la akulu, ananena wina ndi mnzace,

16 kuti, Tidzawacitira ciani anthu awa? pakutitu caoneka kwa onse akukhala m'Yerusalemu kuti cizindikilo cozindikirika cacitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.

17 Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu ali yense, kuti cisabukenso kwa anthu.

18 Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu.

19 Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;

20 pakuti sitingatheife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.

21 Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, cifukwa ca anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu cifukwa ca comwe cidacitika.

22 Pakuti anali wa zaka zace zoposa makumi anai munthuyo, amene cizindikilo ici cakumciritsa cidacitidwa kwa iye.

Okhulupirira athamangira kupemphera

23 Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza ziri zonse oweruza ndi akulu adanena nao.

24 Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse ziri m'menemo;

25 amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davine mtumiki wanu, mudati,Amitundu anasokosera cifukwaciani?Nalingirira zopanda pace anthu?

26 Anadzindandalitsa mafumu a dziko,Ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi,Kutsutsana ndi Ambuye, ndi Kristu wace.

27 Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mudzi muno Herode, ndi Pontiyo Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kumcitira coipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;

28 kuti acite ziri zonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zicitike.

29 Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,

30 m'mene mutambasula dzanja lanu kukaciritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zicitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.

31 Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.

Madyerano a Akristu oyamba

32 Ndipo unyinji wa iwo akukhulupira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka cuma anali naco ndi kace ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

33 Ndipo atumwi anacita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali cisomo cacikuru pa iwo onse.

34 Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; 1 pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ace a izo adazigulitsa,

35 2 nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowakwace.

36 Ndipo Yosefe, wochedwa ndi atumwi Bamaba (ndilo losandulika mwana wa cisangalalo), Mlevi, pfuko lace la ku Kupro,

37 pokhala nao munda, anaugulitsa, nabwera nazo ndalama zace, 3 naziika pa mapazi a atumwi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28