1 Khalani onditsanza ine, monga inenso oditsanza Kristu.
2 Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukila ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.
3 Koma ndifunakuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu,
4 Mwamuna yense wobveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wace.
5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wace; pakuti kuli cimodzimodzi kumetedwa.