24 ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, ici ndi thupi langa la kwa inu; citani ici cikhale cikumbukilo canga.
25 Koteronso cikho, citatha cakudya, ndi kuti, Cikho ici ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; citani ici, nthawi zonse mukamwa, cikhale cikumbukilo canga,
26 Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera cikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.
27 Cifukwa cace yense amene akadyamkate, kapena akamwera cikho ca Ambuye kosayenera, adzakhala wocimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.
28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera cikho.
29 Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa ciweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.
30 Cifukwa cace ambiri mwa inu afoka, nadwala, ndipo ambiri agona.