5 Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wobvula mutu, anyoza mutu wace; pakuti kuli cimodzimodzi kumetedwa.
6 Pakuti ngati mkazi sapfunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kucititsa manyazi, apfunde,
7 Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.
8 Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;
9 pakutinso mwamuna sanalengedwa cifukwa ca mkazi;
10 koma mkazi cifukwa ca mwamuna; cifukwa ca ici mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pace, cifukwa ca angelo.
11 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.