10 ndi kwa wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.
11 Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.
12 Pakuti monga thupi liri limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, ziri thupi limodzi; momwemonso Kristu.
13 Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse rinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.
14 Pakutinso thupisilikhala ciwalo cimodzi, koma zambiri.
15 Ngati phazi likati, Popeza sindiri dzanja, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?
16 Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindiri diso, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?