1 Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe cikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe.
3 Ndipo ndingakhale ndipereka cuma cangaconsekudyetsa osauka, ndipo ndingakhalendipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndiribe cikondi, sindipindula kanthu ai.
4 Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,
5 sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;
6 sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;